1
1 MAFUMU 18:37
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.
Compare
Explore 1 MAFUMU 18:37
2
1 MAFUMU 18:36
Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.
Explore 1 MAFUMU 18:36
3
1 MAFUMU 18:21
Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Explore 1 MAFUMU 18:21
4
1 MAFUMU 18:38
Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mumchera.
Explore 1 MAFUMU 18:38
5
1 MAFUMU 18:39
Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.
Explore 1 MAFUMU 18:39
6
1 MAFUMU 18:44
Ndipo kunali kachisanu ndi chiwiri anati, Taonani, kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani galeta, tsikani, mvula ingakutsekerezeni.
Explore 1 MAFUMU 18:44
7
1 MAFUMU 18:46
Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m'chuuno mwake, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.
Explore 1 MAFUMU 18:46
8
1 MAFUMU 18:41
Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo wa mvula yambiri.
Explore 1 MAFUMU 18:41
9
1 MAFUMU 18:43
Ndipo anati kwa mnyamata wake, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.
Explore 1 MAFUMU 18:43
10
1 MAFUMU 18:30
Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.
Explore 1 MAFUMU 18:30
11
1 MAFUMU 18:24
Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anavomera, nati, Ndiwo mau abwino amene.
Explore 1 MAFUMU 18:24
12
1 MAFUMU 18:31
Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.
Explore 1 MAFUMU 18:31
13
1 MAFUMU 18:27
Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.
Explore 1 MAFUMU 18:27
14
1 MAFUMU 18:32
Ndipo ndi miyalayi anamanga guwa la nsembe m'dzina la Yehova, nazunguniza guwalo ndi mchera, ukulu wake ngati kulandira miyeso iwiri ya mbeu kuzinga guwalo.
Explore 1 MAFUMU 18:32
Home
Bible
Plans
Videos