1
1 MAFUMU 17:14
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.
Compare
Explore 1 MAFUMU 17:14
2
1 MAFUMU 17:1
Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.
Explore 1 MAFUMU 17:1
3
1 MAFUMU 17:13
Ndipo Eliya anati kwa iye, Usachita mantha, kachite monga umo wanenamo, koma thanga wandiocherako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.
Explore 1 MAFUMU 17:13
4
1 MAFUMU 17:12
Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.
Explore 1 MAFUMU 17:12
5
1 MAFUMU 17:9
Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Sidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.
Explore 1 MAFUMU 17:9
6
1 MAFUMU 17:16
Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinachepa, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.
Explore 1 MAFUMU 17:16
7
1 MAFUMU 17:15
Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ake, masiku ambiri.
Explore 1 MAFUMU 17:15
8
1 MAFUMU 17:10
Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'chikho, ndimwe.
Explore 1 MAFUMU 17:10
9
1 MAFUMU 17:4
Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makungubwi kukudyetsa kumeneko.
Explore 1 MAFUMU 17:4
10
1 MAFUMU 17:11
Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.
Explore 1 MAFUMU 17:11
11
1 MAFUMU 17:6
Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
Explore 1 MAFUMU 17:6
12
1 MAFUMU 17:7
Ndipo kunachitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.
Explore 1 MAFUMU 17:7
13
1 MAFUMU 17:24
Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona.
Explore 1 MAFUMU 17:24
14
1 MAFUMU 17:5
Momwemo iye anamuka, nachita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordani.
Explore 1 MAFUMU 17:5
15
1 MAFUMU 17:22
Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.
Explore 1 MAFUMU 17:22
Home
Bible
Plans
Videos