1
1 MAFUMU 19:12
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.
Compare
Explore 1 MAFUMU 19:12
2
1 MAFUMU 19:4
Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.
Explore 1 MAFUMU 19:4
3
1 MAFUMU 19:11
Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime pa phiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho.
Explore 1 MAFUMU 19:11
4
1 MAFUMU 19:13
Ndipo atamva Eliya, anafunda nkhope yake ndi chofunda chake, natuluka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya?
Explore 1 MAFUMU 19:13
5
1 MAFUMU 19:9
Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya?
Explore 1 MAFUMU 19:9
6
1 MAFUMU 19:8
Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu.
Explore 1 MAFUMU 19:8
7
1 MAFUMU 19:5
Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.
Explore 1 MAFUMU 19:5
8
1 MAFUMU 19:7
Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakulaka.
Explore 1 MAFUMU 19:7
9
1 MAFUMU 19:10
Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.
Explore 1 MAFUMU 19:10
10
1 MAFUMU 19:6
Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi.
Explore 1 MAFUMU 19:6
11
1 MAFUMU 19:2
Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe yino.
Explore 1 MAFUMU 19:2
12
1 MAFUMU 19:18
Ndiponso ndidasiya m'Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampsompsona ndi milomo yao.
Explore 1 MAFUMU 19:18
13
1 MAFUMU 19:19
Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.
Explore 1 MAFUMU 19:19
14
1 MAFUMU 19:21
Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.
Explore 1 MAFUMU 19:21
15
1 MAFUMU 19:20
Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndithange ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji?
Explore 1 MAFUMU 19:20
Home
Bible
Plans
Videos