Gen. 14
14
Abramu apulumutsa Loti
1Masiku amenewo, Amurafere mfumu ya ku Sinara, Ariyoki mfumu ya ku Elasara, Kedorilaomere mfumu ya ku Elamu, ndi Tidala mfumu ya ku Goimu, 2onseŵa adasonkhana kuti athire nkhondo mafumu asanu aŵa: Mfumu Bera wa ku Sodomu, mfumu Birisa wa ku Gomora, mfumu Sinabe wa ku Adima, mfumu Semebera wa ku Zeboimu ndi mfumu ya ku Bela (ndiye kuti Zowari). 3Mafumu asanu ameneŵa adasonkhana pamodzi ndi ankhondo ao onse m'chigwa cha Sidimu, (ku Nyanja Yakufa). 4Kedorilaomere ndiye ankalamulira onseŵa pa zaka khumi ndi ziŵiri, koma chaka chakhumi ndi chitatu onseŵa adamuukira. 5Pa chaka chakhumi ndi chinai Kedorilaomere pamodzi ndi anzake ogwirizana nawo, adadza ndi nkhondo nagonjetsa Arefaimu amene ankakhala ku Asiteroti-karanaimu, Azuzimu amene ankakhala ku Hamu, ndi Aemimu amene ankakhala ku chigwa cha Kiriyataimu. 6Adagonjetsanso Ahori amene ankakhala m'mapiri a Seiri mpaka ku Eliparani ku malire a chipululu. 7Ndipo adapotoloka, nakafika ku Enimisipati (ndiye kuti Kadesi), ndipo adagonjetsa dziko lonse la Aamaleke pamodzi ndi la Aamori amene ankakhala ku Hazazoni-Tamara.
8Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi Bela adasonkhanitsa ankhondo ao m'chigwa cha Sidimu, nalimbana 9ndi Kedorilaomere wa ku Elamu, Tidala wa ku Goimu, Amurafere wa ku Sinara ndi Ariyoki wa ku Elasara, mafumu asanu kulimbana ndi mafumu anai. 10Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje a phula. Tsono anthu a ku Sodomu ndi Gomora adagonja nathaŵa nkhondo, ndipo adagwa m'maenjemo, koma ena adathaŵira ku mapiri. 11Mafumu anai aja adatenga zonse za ku Sodomu ndi za ku Gomora, pamodzi ndi chakudya, nachokapo. 12Adamtenganso Loti, mphwake wa Abramu uja, pamodzi ndi zake zonse, chifukwa ankakhala ku Sodomu komweko.
13Koma munthu wina atapulumuka, adabwera kwa Abramu Muhebri uja, namuuza zonsezi. Abramuyo ankakhala pafupi ndi mitengo ija ya thundu ya ku Mamure, wa fuko la Amoni, mbale wa Esikolo ndi Anere, amene ankagwirizana ndi Abramu pa nkhondo. 14Abramu atamva kuti mbale wake wagwidwa, adasonkhanitsa anthu ake odziŵa kumenya nkhondo. Onse pamodzi analipo 318, ndipo adalondola mafumu aja njira yonse mpaka ku Dani. 15Atafika kumeneko, adagaŵa anthu ake m'magulu, ndipo iye ndi anthu ake adakamenyana nawo ndi usiku mpaka kuŵagonjetseratu. Adaŵapirikitsa mpaka ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko, 16ndipo adaŵalanda zao zonse. Adabwera naye Loti, mwana wa mbale wake, pamodzi ndi zake zonse, kuphatikizapo akazi ndi anthu ena onse.
Melkizedeki adalitsa Abramu
17Pamene Abramu ankabwera kuchokera kumene adakagonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu ena ogwirizana naye aja, mfumu ya ku Sodomu idatuluka kukakumana naye ku Chigwa cha Save (ndiye kuti Chigwa cha Mfumu). 18#Ahe. 7.1-10 Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga buledi ndi vinyo. 19Adadalitsa Abramuyo, adati,
“Mulungu Wopambanazonse,
Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi,
akudalitse iwe Abramu.
20Atamandike Mulungu Wopambanazonse,
amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.”
Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zonse zimene adaalanda. 21Komanso mfumu ya ku Sodomu idapempha Abramu kuti “Zinthu zonse mudatengazi, musunge, koma anthu anga okhaŵa mundipatse.” 22Koma Abramu adayankha kuti, “Ndikulumbira pamaso pa Chauta, Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi 23kuti sindidzatenga zinthu zako mpang'ono pomwe. Sindidzatenga ngakhale mbota kapena chingwe chomangira nsapato, kuti ungamadzanene kuti, ‘Abramu ndidamulemeza ndine.’ 24Sinditenga kalikonse ai. Nditengako zokhazo zimene anyamata anga adadya, ndi zoyenera kugaŵira amene adandiperekeza, monga Anere, Esikolo ndi Mamure. Iwo atengeko magawo ao.”
Attualmente Selezionati:
Gen. 14: BLY-DC
Evidenziazioni
Condividi
Copia
Vuoi avere le tue evidenziazioni salvate su tutti i tuoi dispositivi?Iscriviti o accedi
Bible Society of Malawi