Logo YouVersion
Icona Cerca

Gen. 15

15
Mulungu achita chipangano ndi Abramu
1Zitatha izi, Chauta adaonekera Abramu m'masomphenya namuuza kuti, “Usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.” 2Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, ine ndilibe ana. Tsono mungathe bwanji kundipatsa mphotho? Woloŵa m'malo mwanga ndi Eliyezere wa ku Damasikoyu. 3Simudandipatse ana, motero mmodzi mwa akapolo anga ndiye amene adzalandire chuma changa kuti chikhale choloŵa chake.” 4Tsono Chauta adamuuza kuti, “Uyu sadzalandira chuma chako kukhala choloŵa chake. Yemwe adzalandire chuma chakochi ndi mwana wako weniweni.” 5#Aro. 4.18; Ahe. 11.12 Pomwepo Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “Tayang'ana kuthamboku, ndipo uŵerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.” 6#1Am. 2.52; Aro. 4.3; Aga. 3.6; Yak. 2.23Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama.
7Tsono Chauta adamuuza kuti, “Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, kuti ndikupatse dziko lino kuti likhale lakolako.” 8Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, kodi ndingadziŵe bwanji kuti dziko limeneli lidzakhaladi langa?” 9Chauta adamuyankha kuti, “Tandipatsa ng'ombe ya zaka zitatu, mbuzi ya zaka zitatu, nkhosa ya zaka zitatu, ndiponso njiŵa ndi nkhunda.” 10Abramu adabwera nazo nyama zonsezo kwa Mulungu, naziduladula pakati. Adaika mabanduwo aŵiriaŵiri mopenyanapenyana, m'mizere iŵiri. Koma mbalame zija sadazidule. 11Miphamba idadzatera kuti idye nyama zimene adaaphazo, koma Abramu adaipirikitsa.
12 # Yob. 4.13, 14 Pamene dzuŵa linkaloŵa, Abramu adagwidwa ndi tulo tofanato, ndiponso adachita mantha kwambiri. 13#Eks. 1.1-14; Ntc. 7.6 Chauta adamuuza kuti, “Udziŵe ndithu kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni. Zidzakhala akapolo kumeneko, ndipo zidzazunzika zaka zokwanira 400. 14#Eks. 12.40, 41; Ntc. 7.7 Koma mtundu umene udzachite zimenezi, ndidzaulanga, ndipo zidzukulu zakozo potuluka m'dzikomo, zidzatenga chuma chambiri. 15Tsono iwe udzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali ndipo udzafa mwamtendere. Udzaikidwa m'manda utakalamba kwambiri. 16Patapita mibadwo inai, zidzukulu zakozo zidzabwereranso, chifukwa sindidzaŵathamangitsa Aamori mpaka kuipa kwao kutafika pachimake penipeni kuti adzalangidwe.”
17Dzuŵa litangoloŵa, kachisisira katagwa, mwadzidzidzi padaoneka mphika wogaduka ndi moto, pamodzi ndi nsakali yoyaka, ndipo ziŵirizi zidadutsa pakati pa nyama zodulidwa zija. 18#Ntc. 7.5 Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. 19Ndidzakupatsa dziko la Akeni, la Akenizi, la Akadimoni, 20la Ahiti, la Aperizi, la Arefaimu, 21la Aamori, la Akanani, la Agirigasi ndi la Ayebusi.”

Attualmente Selezionati:

Gen. 15: BLY-DC

Evidenziazioni

Condividi

Copia

None

Vuoi avere le tue evidenziazioni salvate su tutti i tuoi dispositivi?Iscriviti o accedi