1
Gen. 14:20
Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa
Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zonse zimene adaalanda.
Confronta
Esplora Gen. 14:20
2
Gen. 14:18-19
Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga buledi ndi vinyo. Adadalitsa Abramuyo, adati, “Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu.
Esplora Gen. 14:18-19
3
Gen. 14:22-23
Koma Abramu adayankha kuti, “Ndikulumbira pamaso pa Chauta, Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi kuti sindidzatenga zinthu zako mpang'ono pomwe. Sindidzatenga ngakhale mbota kapena chingwe chomangira nsapato, kuti ungamadzanene kuti, ‘Abramu ndidamulemeza ndine.’
Esplora Gen. 14:22-23
Home
Bibbia
Piani
Video