Ntc. 8
8
1Saulo uja ankavomerezana nawo za kupha kumeneku.
Saulo ayamba kuzunza Mpingo
Tsiku limenelo mpingo wa ku Yerusalemu udayamba kuzunzidwa kwambiri, ndipo onse, kupatula atumwi okha, adabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya. 2Anthu ena okonda Mulungu adakaika maliro a Stefano namlira kwambiri.
3 #
Ntc. 22.4, 5; 26.9-11 Koma Saulo uja ankapasula Mpingo. Ankaloŵa m'nyumba za anthu, namagwira amuna ndi akazi omwe, nkumaŵaponya m'ndende.
Filipo akalalika Uthenga Wabwino ku Samariya
4Okhulupirira amene adabalalika aja adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino. 5Filipo adatsikira ku mzinda wa ku Samariya, namalalikira anthu akumeneko za Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja. 6Makamu a anthu ndi mtima umodzi ankatchera makutu ku zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera mau ake nkumaona zozizwitsa zimene iye ankachita. 7Pakuti mizimu yonyansa inkatuluka mwa anthu ambiri amene anali atagwidwa nayo, nimafuula kwambiri. Ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo kapena opunduka, ankachira. 8Choncho munali chimwemwe chachikulu mumzinda muja.
Za Simoni wamatsenga
9Koma mumzindamo munali munthu wina, dzina lake Simoni amene kale ankachita matsenga, namadodometsa anthu onse a ku Samariyako. Iyeyu ankadzimveketsa kuti ndi munthu wamkulu. 10Anthu onse, aang'ono ndi aakulu omwe, ankamumvera namamtsata nkumanena kuti, “Munthu ameneyu ndiye mphamvu ya Mulungu ija amati, Mphamvu yaikulu.” 11Ankamutsata chifukwa pa nthaŵi yaitali ankaŵadodometsa ndi matsenga akewo. 12Koma pamene Filipo ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ndiponso za dzina la Yesu Khristu, anthu adakhulupirira, ndipo adabatizidwa, amuna ndi akazi omwe. 13Simoni uja nayenso adakhulupirira, ndipo atabatizidwa, ankakhalira limodzi ndi Filipo. Adazizwa pakuwona zizindikiro ndi zozizwitsa zimene zinkachitika.
14Pamene atumwi okhala ku Yerusalemu adamva kuti anthu a ku Samariya alandira mau a Mulungu, adatumako Petro ndi Yohane. 15Iwowo atafika, adayamba kupempherera okhulupirira aja kuti alandire Mzimu Woyera. 16Nthaŵiyo nkuti Mzimu Woyera asanafike pa wina aliyense mwa iwo. Onsewo anali atangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. 17Tsono Petro ndi Yohane adaŵasanjika manja, ndipo adalandira Mzimu Woyera.
18Simoni uja ataona kuti Mzimu Woyera waperekedwa kwa iwo atumwi aja ataŵasanjika manja, adafuna kuŵapatsa ndalama atumwiwo. 19Adati, “Bwanji mutandipatsako inenso mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndikamsanjike manja, akalandire Mzimu Woyera.” 20Petro adamuyankha kuti, “Ndalama zakozo ukatayike nazo pamodzi. Iwe ukuganiza kuti ungathe kupata mphatso ya Mulungu pakupereka ndalama kodi? 21Ulibe gawo kapena malo pa ntchito imeneyi, pakuti mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu. 22Nchifukwa chake tembenuka mtima, uleke choipa chakochi. Pempha Ambuye kuti mwina mwake nkukukhululukira maganizo a mumtima mwakoŵa. 23Pakuti ndakuwona kuti ndiwe wodzaza ndi ndulu yoŵaŵa, ndiponso ndiwe womangidwa ndi maunyolo a zoipa.” 24Apo Simoni uja adati, “Mundipempherere inuyo kwa Ambuye kuti zimene mwanenazi zisandigwere.”
25Petro ndi Yohane atatha kupereka umboni wao ndi kulalika mau a Ambuye, adabwerera ku Yerusalemu. Ankapita nalalika Uthenga Wabwino m'midzi yambiri ya Asamariya.
Za Filipo ndi nduna ya za chuma ya ku Etiopiya
26Mngelo wa Ambuye adauza Filipo kuti, “Nyamuka, pita chakumwera, kutsata mseu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu; mseu wodzera m'chipululu uja.” 27Filipo adanyamukadi napita. Ndipo munthu wina wa ku Etiopiya adaabwera ku Yerusalemu kudzapembedza. Iyeyu anali nduna yaikulu ya m'banja la mfumukazi Kandake wa ku Etiopiya, ndiponso woyang'anira chuma chake chonse. 28Nthaŵi imeneyo ankabwerera kwao. Anali pa galeta akuŵerenga buku la mneneri Yesaya. 29Tsono Mzimu Woyera adauza Filipo kuti, “Pita, kayandikane nalo galetalo.” 30Filipo adathamangira nduna ija, ndipo adaimva ikuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono adaifunsa kuti, “Bwana, kodi mukumvetsa zimene mukuŵerengazi?” 31Iye adati, “Ha, ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Motero adaitana Filipo kuti adzakwere ndi kukhala naye pagaletapo. 32#Yes. 53.7, 8 Mau a m'Malembo amene ankaŵerengawo ndi aŵa:
“Iye anali ngati nkhosa yoitsogoza pokaipha,
ngati mwana wankhosa wongokhala duu pomumeta.
Sadalankhulepo kanthu.
33Adampeputsa,
pa mlandu wake sadamchitire chilungamo.
Palibe amene adzatha kusimba za zidzukulu zake,
pakuti moyo wake wachotsedwa pa dziko lapansi.”
34Pamenepo nduna ija idati, “Pepani, tandiwuzani, kodi zimenezi mneneriyo akunena za yani, za iye mwini, kapena za wina?” 35Apo Filipo adayamba kumlalikira Uthenga Wabwino wa Yesu kuyambira pa Malembo ameneŵa. 36Ndipo pamene ankapita mumseumo, adafika pena pamene panali madzi. Nduna ija idati, “Madzi si aŵa. Monga pali choletsa kuti ndisabatizidwe?”
[ 37Filipo adayankha kuti, “Mungathe kubatizidwa ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse.” Iye adati, “Ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.”] 38Pamenepo ndunayo idalamula kuti galetalo liime. Aŵiri onsewo, Filipo ndi nduna ija, adatsikira ku madzi, Filipo nkumubatiza. 39Pamene adatuluka m'madzimo, Mzimu wa Ambuye adamchotsapo Filipo uja. Ndipo nduna ija siidamuwonenso, koma idapitirira ulendo wake ikusangalala. 40Tsono Filipo adapezeka kuti ali ku Azoto. Adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino m'mizinda yonse, mpaka adakafika ku Kesareya.
Currently Selected:
Ntc. 8: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi