YouVersion Logo
Search Icon

Ntc. 7

7
Mau a Stefano
1Mkulu wa ansembe onse adafunsa Stefano kuti, “Kodi zimenezi nzoona?” 2#Gen. 12.1 Iye adayankha kuti, “Abale anga ndi atate anga, mverani! Mulungu waulemerero adaonekera kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani. 3Adamuuza kuti, ‘Tuluka m'dziko lako, uŵasiye abale ako, ubwere ku dziko limene ndidzakusonyeza.’ 4#Gen. 11.31; Gen. 12.4Tsono adatulukadi m'dziko la Akaldeya nakakhala ku Harani. Bambo wake atamwalira, Mulungu adamchotsa kumeneko, nakamufikitsa ku dziko lino kumene inu mukukhala tsopano. 5#Gen. 12.7; 13.15; 15.18; 17.8 Mulungu sadampatseko ndi kadera kakang'onong'ono komwe ka dzikoli kuti kakhale kakekake. Koma adamlonjeza kuti adzampatsa dzikoli kuti likhale lakelake ndiponso la zidzukulu zake, ngakhale pa nthaŵi imeneyo nkuti akadalibe mwana. 6#Gen. 15.13, 14Mulungu adati, ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo ku dziko lina kumene eniake adzaziyesa akapolo, nadzazizunza pa zaka mazana anai.’ 7#Eks. 3.12 Mulungu adatinso, ‘Koma Ine ndidzaulanga mtundu wa anthuwo umene udzazisandutsa akapolo. Bwino lake zidzatuluka m'dzikomo nkudzandipembedza pamalo pano.’ 8#Gen. 17.10-14; Gen. 21.2-4; Gen. 25.26; Gen. 29.31—35.18 Tsono Mulungu adachita chipangano ndi Abrahamu, chimene chizindikiro chake chinali kuumbala. Motero Abrahamu adaumbala mwana wake Isaki, ali ndi masiku asanu ndi atatu akubadwa. Isaki adaumbala Yakobe, ndipo Yakobe adaumbala makolo athu khumi ndi aŵiri#7.8: makolo athu khumi ndi aŵiri: Ameneŵa ndi ana a Yakobe (Gen. 29.31—30.24). aja.
9 # Gen. 37.11; Gen. 37.28; Gen. 39.2, 21 “Tsono makolo athuwo adachita nsanje ndi mbale wao Yosefe, ndipo adamgulitsa kuti akakhale kapolo ku Ejipito. Koma Mulungu anali naye, 10#Gen. 41.39-41mwakuti adampulumutsa ku masautso ake onse. Adampatsa nzeru ndi kumkometsa pamaso pa Farao, mfumu ya ku Ejipito, kotero kuti mfumuyo idamuika kuti akhale nduna yaikulu ya dziko la Ejipito, ndiponso woyang'anira banja lake lonse. 11#Gen. 42.1, 2 Koma mudadzaloŵa njala m'dziko lonse la Ejipito, ndiponso m'Kanani, kotero kuti anthu adazunzika kwambiri. Makolo athu omwe sadathe kupeza chakudya. 12Pamene Yakobe adamva kuti ku Ejipito kuli tirigu, adatumako makolo athu aja. Uwu unali ulendo wao woyamba. 13#Gen. 45.1; Gen. 45.16 Pa ulendo wachiŵiri Yosefe adadziwulula kwa abale akewo, ndipo adadziŵitsa Farao za banja lonselo. 14#Gen. 45.9, 10, 17, 18; Gen. 46.27Tsono Yosefe adaitanitsa Yakobe, bambo wake, pamodzi ndi banja lake lonse. Onse pamodzi anali anthu 75. 15#Gen. 46.1-7; Gen. 49.33 Motero Yakobe adapita ku Ejipito, iye ndi makolo athu omwe aja. Onsewo adakamwalira kumeneko. 16#Gen. 23.3-16; 33.19; 50.7-13; Yos. 24.32 Pambuyo pake iye adaŵanyamula kupita nawo ku Sekemu, kumene adaŵaika m'manda amene Abrahamu adaagula ndi ndalama kwa ana a Hamori ku Sekemu.
17 # Eks. 1.7, 8 “Pamene idayandikira nthaŵi yakuti Mulungu achite zimene adaalonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu udakula ndi kuchuluka ku Ejipito. 18Pambuyo pake mfumu ina imene sidadziŵe Yosefe, idayamba kulamulira ku Ejipito. 19#Eks. 1.10, 11; Eks. 1.22 Mfumuyo idachenjerera mtundu wathu, nkuyamba kuzunza makolo athu, pakuŵatayitsa ana ao akhanda kuti asakhale ndi moyo. 20#Eks. 2.2 Nthaŵi imeneyo Mose adabadwa, ndipo anali mwana wokongola kwambiri. Adamlera kwao miyezi itatu, 21#Eks. 2.3-10koma atamsiya pamtsinje paja, mwana wamkazi wa Farao adamtola, namlera ngati mwana wake. 22Motero Mose adaphunzira nzeru zonse za anthu a ku Ejipito, ndipo mau ake ndi ntchito zake zinali zamphamvu.
23 # Eks. 2.11-15 “Pamene zaka zake zidafikira makumi anai, adaganiza zokayendera abale ake, Aisraele. 24Tsono pamene adaona kuti Mwejipito wina akuzunza mmodzi mwa abale akewo, Moseyo adatchinjiriza Mwisraeleyo, nalipsira Mwejipito uja pakumupha. 25Iye ankaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu adamuika kuti adzaŵapulumutse, koma iwo sadazindikire. 26M'maŵa mwake atabwera, adapeza Aisraele aŵiri akumenyana. Adayesa kuŵayanjanitsa pakuŵauza kuti, ‘Anthuni, muli pa chibale, bwanji mukuvutana?’ 27Koma amene adaaputa mnzakeyo adakankhira Mose kumbali nati, ‘Adakuika ndani kuti ukhale mkulu wathu ndi muweruzi wathu? 28Kodi ukufuna kuphanso ine monga udaphera Mwejipito dzulo lija?’ 29#Eks. 18.3, 4Pamene Mose adamva mau ameneŵa, adathaŵa namakakhala ku chilendo ku dziko la Midiyani. Kumeneko adabereka ana aamuna aŵiri.
30 # Eks. 3.1-10 “Tsono patapita zaka makumi anai, mngelo adaonekera Mose ku chipululu cha ku phiri la Sinai, m'malaŵi a moto pa chitsamba. 31Mose ataona zimenezi adazizwa, ndipo adasendera pafupi kuti aonetsetse. Pamenepo adamva mau a Chauta akuti, 32‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Yakobe.’ Mose adayamba kunjenjemera mwakuti sadalimbenso mtima kuti nkupenyako. 33Apo Chauta adamuuza kuti, ‘Vula nsapato zakozo, chifukwa malo ukupondawo ngopatulika. 34Ndaona ndithu kuvutika kwa anthu anga amene ali ku Ejipito. Ndamva kudandaula kwao, ndipo ndabwera kudzaŵapulumutsa. Tiye tsopano, ndikutume ku Ejipito.’
35 # Eks. 2.14 “Moseyo ndi yemwe uja amene Aisraele aja adaamkana nkumanena kuti, ‘Adakuika ndani kuti ukhale mkulu wathu ndi muweruzi wathu?’ Yemweyo Mulungu adamtuma kuti akhale mkulu ndi momboli kudzera mwa mngelo uja amene adaamuwonekera pa chitsamba. 36#Eks. 7.3; Eks. 14.21; Num. 14.33 Moseyo ndiye adaŵatsogolera anthuwo naŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ankachita zozizwitsa ndi zizindikiro ku Ejipito, pa Nyanja Yofiira, ndiponso m'chipululu zaka makumi anai. 37#Deut. 18.15, 18 Mose yemweyo ndiye amene adauza Aisraele kuti, ‘Mulungu adzatuma wina kuchokera mwa abale anu kuti akhale Mneneri wanu monga ine.’ 38#Eks. 19.1—20.17; Deut. 5.1-33Moseyo ndi yemwe uja amene anali nao pa msonkhano wa Aisraele m'chipululu. Iye adaaimirira pakati pa makolo athu ndi mngelo uja amene adalankhula naye ku phiri la Sinai. Ndiye amene adalandira mau opatsa moyo kuti adzatininkhe ife.
39“Koma makolo athu aja adakana kumumvera, m'malo mwake adamkankhira kumbali. Mitima yao idatembenukira za ku Ejipito. 40#Eks. 32.1Choncho adauza Aroni kuti, ‘Tipangireni milungu kuti izititsogolera, pakuti sitikudziŵa chimene chamgwera Mose uja, amene adatitsogolera potuluka m'dziko la Ejipito.’ 41#Eks. 32.2-6Tsono masiku amenewo iwo adapanga fano la mwanawang'ombe. Adapereka nsembe kwa fanoli, nakondwerera ntchito za manja ao. 42#Amo. 5.25-27 Pamenepo Mulungu adaŵafulatira, naŵapereka ku machimo akupembedza nyenyezi, monga akunenera mau olembedwa m'buku la aneneri kuti,
“ ‘Inu Aisraele, musayese kuti munkapereka kwa Ine
nyama zimene munkapha ndi kuzipereka ngati nsembe
pa zaka makumi anai zija m'chipululu.
43Munkanyamula hema la Moleki,
ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani,#7.43: Moleki...Refani: Imeneyi ndi milungu yachilendo, imene anthu a ku Kanani ankapembedza kale.
mafano amene mudaŵapanga
kuti muziŵapembedza.
Ndidzakuchotsani kukutayani kutali,
kupitirira dziko la Babele.’
44 # Eks. 25.9, 40 “Makolo athu anali ndi chihema cha umboni m'chipululu muja. Adachipanga monga momwe Mulungu adaauzira Mose ndiponso molingana ndi chithunzi chimene Mose adaachiwona. 45#Yos. 3.14-17 Chihemacho chimene makolo athu adachilandira kwa makolo ao aja, adabwera nacho kuno Yoswa akuŵatsogolera pamene adalanda dziko kwa mitundu ya anthu imene Mulungu adaipitikitsa iwo akufika. Chidakhala pakati pao mpaka nthaŵi ya Davide. 46#2Sam. 7.1-16; 1Mbi. 17.1-14 Davideyo, Mulungu adamkomera mtima, ndipo adapempha Mulunguyo kuti amlole kumangira nyumba Iye amene ali Mulungu wa Yakobe. 47#1Maf. 6.1-38; 2Mbi. 3.1-17 Koma Solomoni ndiye adammangira nyumbayo. 48Ngakhale zinali choncho Mulungu Wopambanazonse sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja, monga akunenera mneneri kuti,
49 # Yes. 66.1, 2 “Chauta akuti,
‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu,
dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.
Kodi mudzandimangira nyumba yotani?
Kapena malo opumuliramo Inewo ngotani?
50Kodi si manja anga omwe amene adapanga zonsezi?’ ”
51 # Yes. 63.10 Stefano adapitirira nati, “Ha, anthu okanika inu, mitima yanu njachikunja, makutu anu ngogontha. Nthaŵi zonse, monga ankachitira makolo anu, inunso mumakana kumvera Mzimu Woyera. 52Kodi alipo mneneri ndi mmodzi yemwe amene makolo anu aja sadamzunze? Iyai, iwo adapha anthu amene ankaneneratu za kudza kwake kwa Wolungama uja.#7.52: Wolungama uja: Ameneyu ndi Yesu. Tsopano inuyo mudampereka kwa adani ake ndi kumupha. 53Inu mudaalandira Malamulo a Mulungu kudzera mwa angelo, komabe simudaŵasunge konse.”
Ayuda amponya miyala Stefano
54Pamene abwalo aja adamva mau a Stefanowo, adakwiya kwabasi, namchitira tsinya. 55Koma Stefano, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adayang'ana kumwamba naona ulemerero wa Mulungu, ndiponso Yesu ataimirira ku dzanja lamanja#7.55: ku dzanja lamanja: Ndiye kuti malo aulemu. la Mulungu. 56Tsono adati, “Onani! Ndikuwona Kumwamba kotsekuka, ndipo Mwana wa Munthu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.” 57Koma iwo adafuula kwambiri, natseka m'makutu mwao, namgudukira onse pamodzi. 58Adamtulutsira kunja kwa mzinda, nakamponya miyala. Mboni zidasungiza zovala zao munthu wachinyamata wina, dzina lake Saulo. 59Pamene anthuwo ankamuponya miyala, Stefano adayamba kupemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” 60Ndipo adagwada pansi nafuula kwakukulu kuti, “Ambuye, musaŵaŵerengere tchimoli.” Atanena mau ameneŵa, adafa.

Currently Selected:

Ntc. 7: BLY-DC

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in