Tsono Mzimu Woyera adauza Filipo kuti, “Pita, kayandikane nalo galetalo.” Filipo adathamangira nduna ija, ndipo adaimva ikuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono adaifunsa kuti, “Bwana, kodi mukumvetsa zimene mukuŵerengazi?” Iye adati, “Ha, ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Motero adaitana Filipo kuti adzakwere ndi kukhala naye pagaletapo.