Ntc. 9
9
Saulo atembenuka mtima
1Saulo uja ankaopsezabe ophunzira a Ambuye, nkumafuna kuŵapha. Adapita kwa mkulu wa ansembe onse 2kukampempha makalata opita nawo ku nyumba zamapemphero za ku Damasiko. Ankafuna kuti ngati akapezeko ena otsata Njira ya Ambuye, kaya ndi amuna kaya ndi akazi, akaŵamange nkubwera nawo ku Yerusalemu.
3Ali paulendo wakewo, adayandikira mzinda wa Damasiko uja. Mwadzidzidzi kuŵala kochokera kumwamba kudamzinga. 4Adagwa pansi namva mau akuti, “Saulo, Saulo, ukundizunziranji Ine?” 5Iye adafunsa kuti, “Ndinu yani, Ambuye?” Iwo adati, “Ndine Yesu amene ukundizunza. 6Koma dzuka, kaloŵe mumzindamo, ndipo akakuuza chochita.” 7Anthu amene anali naye pa ulendowo adaima, atangoti chete. Mauwo ankaŵamva, koma osaona munthu. 8Saulo adadzuka, koma pamene maso ake adaphenyuka, sadathe kupenya kanthu. Tsono anzake aja adamgwira pa dzanja naloŵa naye m'Damasiko. 9Ndipo adakhala masiku atatu osatha kupenya ndiponso osadya kapena kumwa kanthu.
10Tsono ku Damasikoko kunali wophunzira wina, dzina lake Ananiya. Iyeyu adaaona m'masomphenya Ambuye akumuitana kuti, “Ananiya!” Iye adati, “Ee, Ambuye.” 11Apo Ambuye adamuuza kuti, “Nyamuka, upite ku mseu wa mumzindamu umene amati, ‘Njira Yolunjika.’ Ndipo ku nyumba ya Yudasi ukafune munthu wina wa ku Tariso, dzina lake Saulo. Panopa akupemphera, 12ndipo waona m'masomphenya munthu wina, dzina lake Ananiya, akuloŵa ndi kumsanjika manja kuti apenyenso.” 13Atamva zimenezo Ananiya adati, “Ambuye, anthu ambiri andiwuza za munthu ameneyu, kuti adaŵachita zoipa zambiri anthu anu ku Yerusalemu. 14Ndipo wabwera kuno ndi ulamuliro wa akulu a ansembe kuti adzamange onse otama dzina lanu mopemba.” 15Koma Ambuye adamuuza kuti, “Pita, pakuti iyeyu ndi mtumiki wanga amene ndidamsankha kuti akalalikire dzina langa anthu a mitundu ina, mafumu, ndiponso Aisraele. 16Ine ndidzamuwonetsa zoŵaŵa zonse zimene adzayenera kumva chifukwa cha Ine.”
17Pamenepo Ananiya adanyamuka nakaloŵa m'nyumbamo. Adamsanjika manja Sauloyo nati, “Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene adakuwonekera pa njira imene wadzera ija, andituma. Akufuna kuti upenyenso, ndipo udzazidwe ndi Mzimu Woyera.” 18#Tob. 11.13-15Pompo m'maso mwake mudachoka zinthu zonga mamba a nsomba, ndipo adayambanso kupenya. Adaimirira nabatizidwa, 19ndipo atadya chakudya, adapezanso mphamvu.
Saulo ayamba kulalika ku Damasiko
Saulo adakhala masiku angapo limodzi ndi ophunzira a ku Damasiko. 20Ndipo posakhalitsa adayamba kulalika m'nyumba zamapemphero za Ayuda kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
21Anthu onse amene ankamva mau akewo ankadabwa, namafunsana kuti, “Kodi ameneyu si yemwe uja amene ku Yerusalemu ankapha anthu otama dzinali mopemba? Kodi siwabwera kuno kuti aŵamange otereŵa ndi kukaŵapereka kwa akulu a ansembe?” 22Tsono mphamvu za Saulo zinkakulirakulira, ndipo adathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko pakuŵatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Saulo athaŵa Ayuda
23 #
2Ako. 11.32, 33 Patapita masiku ambiri, Ayuda adapangana kuti aphe Saulo, 24koma anthu ena adamuuzako za chiwembucho. Anthu achiwembuwo ankadikira pa zipata za linga la mzinda usana ndi usiku kuti amuphe. 25Koma ophunzira ake adamtenga usiku, namtsitsira kunja kwa lingalo m'dengu.
Saulo ku Yerusalemu
26Saulo atafika ku Yerusalemu, adayesa kuloŵa m'gulu la ophunzira aja. Koma onse adachita naye mantha, osakhulupirira kuti nayenso ndi wophunzira. 27Pamenepo munthu wina, dzina lake Barnabasi, adamtenga napita naye kwa atumwi. Iye adaŵafotokozera za m'mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja, ndipo kuti Ambuye adaalankhula naye. Adaŵasimbiranso za m'mene Saulo ku Damasiko ankalankhulira molimba mtima m'dzina la Yesu. 28Tsono Saulo adakhala nawo, nayendera Yerusalemu yense akulalika molimba mtima m'dzina la Ambuye. 29Ankalankhulanso ndi kumatsutsana ndi Ayuda olankhula Chigriki, koma iwowo ankafunafuna kumupha. 30Pamene abale adamva zimenezi, adapita naye ku Kesareya namtumiza ku Tariso.
31Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adaloŵamo chifukwa anthu ake ankayenda moopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankaŵalimbikitsa.
Petro achiritsa Eneya
32Pamene Petro ankayendera anthu a Mulungu uku ndi uku, adakafika kwa amene ankakhala ku Lida. 33Kumeneko adapezako munthu wina, dzina lake Eneya, amene anali atagona pa mphasa zaka zisanu ndi zitatu, ali wofa ziwalo. 34Tsono Petro adamuuza kuti, “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa. Dzuka, yalula mphasa yako.” Pomwepo iye adadzukadi. 35Anthu onse okhala ku Lida ndi ku Saroni atamuwona, adatembenukira kwa Ambuye.
Petro aukitsa Dorika
36Ku Yopa kunali wophunzira wina wamkazi, dzina lake Tabita (pa Chigriki amati Dorika). Iyeyu ankachita ntchito zabwino zambiri ndi kumathandiza osauka. 37Masiku amenewo maiyo adaadwala, nkumwalira. Anthu adatsuka maliro, nakagoneka mtembo m'chipinda cham'mwamba. 38Ku Yopa kunali kufupi ndi ku Lida, choncho pamene ophunzira adamva kuti Petro ali ku Lida, adatuma anthu aŵiri kuti akamuuze kuti, “Chonde, mubwere kwathu kuno msanga.” 39Tsono Petro adanyamuka napita nawo. Pamene iye adafika, adamperekeza ku chipinda cham'mwamba chija. Akazi onse amasiye adangoti kwete m'mbali mwakemu, akungolira, nkumamuwonetsa malaya ndi zovala zina zimene Dorika ankasoka ali nawo pamodzi. 40Petro adaŵapempha onse kuti atuluke, ndipo adagwada pansi nkumapemphera. Kenaka adatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka!” Apo Tabita adatsekula maso, ndipo pamene adaona Petro, adakhala tsonga.
41Petro adamgwira dzanja namuimiritsa. Ndipo adaitana anthu a Mulungu ndi azimai amasiye aja, nampereka kwa iwo ali wamoyo. 42Anthu onse a ku Yopa adamva zimenezi, ndipo ambiri adakhulupirira Ambuye. 43Tsono Petro adakhala ku Yopa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa.
Currently Selected:
Ntc. 9: BLY-DC
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
Bible Society of Malawi