MASALIMO 90
90
Mulungu ndiye wachikhalire, munthu ndiye wakutha msanga
Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.
1 #
Deut. 33.27
Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo
m'mibadwomibadwo.
2 #
Miy. 8.25-26
Asanabadwe mapiri,
kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu,
inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha,
Inu ndinu Mulungu.
3 #
Gen. 3.19
Mubweza munthu akhale fumbi;
nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.
4 #
2Pet. 3.8
Pakuti pamaso panu zaka zikwi
zikhala ngati dzulo, litapita,
ndi monga ulonda wa usiku.
5 #
Mas. 103.15-16; Yes. 40.6-8 Muwatenga ngati ndi madzi aakulu, akhala ngati tulo;
mamawa akhala ngati msipu wophuka.
6Mamawa uphuka bwino;
madzulo ausenga, nuuma.
7Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu;
ndipo m'kuzaza kwanu tiopsedwa.
8 #
Yer. 16.17; Aheb. 4.13 Munaika mphulupulu zathu pamaso panu,
ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.
9Pakuti masiku athu onse apitirira m'ukali wanu;
titsiriza moyo wathu ngati lingaliro.
10Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri,
kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu;
koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake;
pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
11Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani,
ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?
12 #
Mas. 39.4
Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero,
kuti tikhale nao mtima wanzeru.
13 #
Ower. 2.18
Bwerani, Yehova; kufikira liti?
Ndipo alekeni atumiki anu.
14 #
Mas. 85.6
Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa;
ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.
15Tikondweretseni monga mwa masiku mudatizunzawa,
ndi zaka tidaona choipa.
16 #
Hab. 3.2
Chochita Inu chioneke kwa atumiki anu,
ndi ulemerero wanu pa ana ao.
17 #
Mas. 50.15; Yes. 26.12 Ndipo chisomo chake cha Yehova Mulungu wathu chikhalire pa ife;
ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu;
inde, ntchito ya manja athu muikhazikitse.
Currently Selected:
MASALIMO 90: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi