MASALIMO 91
91
Mulungu asungadi wodzipereka kwa Iye
1 #
Mas. 27.5; 17.8 Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba
adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
2 #
Mas. 142.5
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa;
Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
3 #
Mas. 124.7
Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi,
kumliri wosakaza.
4 #
Mas. 61.4
Adzakufungatira ndi nthenga zake,
ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake;
choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.
5 #
Miy. 3.23-24
Sudzaopa choopsa cha usiku,
kapena muvi wopita usana;
6kapena mliri woyenda mumdima,
kapena chionongeko chakuthera usana.
7Pambali pako padzagwa chikwi,
ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako;
sichidzakuyandikiza iwe.
8 #
Mala. 1.4-5
Koma udzapenya ndi maso ako,
nudzaona kubwezera chilango oipa.
9 #
Mas. 71.3
Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga!
Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako;
10 #
Miy. 12.21
palibe choipa chidzakugwera,
ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.
11 #
Mat. 4.6
Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe,
akusunge m'njira zako zonse.
12Adzakunyamula pa manja ao,
ungagunde phazi lako pamwala.
13Udzaponda mkango ndi mphiri;
udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.
14 #
Mas. 9.10
Popeza andikondadi ndidzampulumutsa;
ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.
15 #
Mas. 27.4
Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha;
kunsautso ndidzakhala naye pamodzi;
ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu.
16Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri,
ndi kumuonetsera chipulumutso changa.
Currently Selected:
MASALIMO 91: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi