YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 89

89
Pangano la Mulungu ndi Davide Mulungu adzapulumutsa anthu ake
Chilangizo cha Etani Mwezara.
1 # Mas. 101.1 Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse,
pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu
ku mibadwomibadwo.
2 # Mas. 119.89-90 Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka;
mudzakhazika chikhulupiriko chanu m'Mwamba mwenimweni.
3 # 2Sam. 7.11-13 Ndinachita chipangano ndi wosankhika wanga,
ndinalumbirira Davide mtumiki wanga.
4Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse,
ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo.
5 # Mas. 97.6 Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova;
chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.
6 # Mas. 71.19 Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova?
Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?
7 # Mas. 76.7, 11 Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri m'upo wa oyera mtima,
ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.
8Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova?
Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.
9 # Mas. 65.7; Mat. 8.26 Inu ndinu wakuchita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja;
pakuuka mafunde ake muwachititsa bata.
10Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa;
munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.
11 # Gen. 1.1; Mas. 24.1-2 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu;
munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.
12Munalenga kumpoto ndi kumwera;
Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m'dzina lanu.
13Muli nao mkono wanu wolimba;
m'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.
14 # Mas. 85.10-11; 97.2 Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wachifumu wanu;
chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.
15 # Mas. 4.6 Odala anthu odziwa liu la lipenga;
ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
16Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse;
ndipo akwezeka m'chilungamo chanu.
17 # Mas. 92.10 Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;
ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.
18Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova;
ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.
19 # Mas. 89.3 Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu,
ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona;
ndakweza wina wosankhika mwa anthu.
20Ndapeza Davide mtumiki wanga;
ndamdzoza mafuta anga oyera.
21Amene dzanja langa lidzakhazikika naye;
inde mkono wanga udzalimbitsa.
22 # 2Sam. 7.9-10 Mdani sadzamuumira mtima;
ndi mwana wa chisalungamo sadzamzunza.
23Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pake;
ndidzapandanso odana naye.
24Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa
zidzakhala naye;
ndipo nyanga yake idzakwezeka m'dzina langa.
25Ndipo ndidzaika dzanja lake panyanja,
ndi dzanja lamanja lake pamitsinje.
26 # 2Sam. 7.14 Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga,
Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.
27 # Mas. 2.7; Akol. 1.15, 18 Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba,
womveka wa mafumu a pa dziko lapansi.
28 # Yes. 55.3 Ndidzamsungira chifundo changa kunthawi yonse,
ndipo chipangano changa chidzalimbika pa iye.
29 # Mas. 89.4, 36 Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire,
ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m'mwamba.
30 # Yer. 9.13-16 Ana ake akataya chilamulo changa,
osayenda m'maweruzo anga,
31nakaipsa malembo anga;
osasunga malamulo anga.
32Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,
ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.
33Koma sindidzamchotsera chifundo changa chonse,
ndi chikhulupiriko changa sichidzamsowa.
34Sindidzaipsa chipangano changa,
kapena kusintha mau otuluka m'milomo yanga.
35Ndinalumbira kamodzi m'chiyero changa;
sindidzanamizira Davide.
36 # 1Maf. 2.4; Yoh. 12.34 Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse,
ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.
37Udzakhazikika ngati mwezi kunthawi yonse,
ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.
38Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza,
munakwiya naye wodzozedwa wanu.
39Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu;
munaipsa korona wake ndi kumponya pansi.
40Munapasula makoma ake onse;
munagumula malinga ake.
41Onse opita panjirapa amfunkhira,
akhala chotonza cha anansi ake.
42Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa;
munakondweretsa adani ake onse.
43Munapinditsa kukamwa kwake kwa lupanga lake,
osamuimika kunkhondo.
44Munaleketsa kuwala kwake,
ndipo munagwetsa pansi mpando wachifumu wake.
45Munafupikitsa masiku a mnyamata wake;
munamkuta nao manyazi.
46 # Mas. 79.5 Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova;
ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?
47 # Yob. 7.7 Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi;
munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?
48Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa?
Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda?
49 # 2Sam. 7.15 Chilikuti chifundo chanu chakale, Ambuye,
munachilumbirira Davide pa chikhulupiriko chanu?
50Kumbukirani, Ambuye, chotonzera atumiki anu;
ndichisenza m'chifuwa mwanga
chochokera kumitundu yonse yaikulu ya anthu.
51 # Mas. 74.22 Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho;
chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu.
52Wodalitsika Yehova kunthawi yonse.
Amen ndi Amen.

Currently Selected:

MASALIMO 89: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in