MASALIMO 88
88
Wa Salimo atchula masautso ake, napempha Mulungu amdalitse kuimfa
Nyimbo, Salimo la ana a Kora. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Mahalati Leanoti. Chilangizo cha Hemani Mwezara.
1 #
Mas. 51.14; Luk. 18.1 Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,
ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.
2Pemphero langa lidze pamaso panu;
munditcherere khutu kukuwa kwanga.
3Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto,
ndi moyo wanga wayandikira kumanda.
4Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;
ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu.
5Wotayika pakati pa akufa,
ngati ophedwa akugona m'manda,
amene simuwakumbukiranso;
ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.
6Munandiika kunsi kwa dzenje,
kuli mdima, kozama.
7 #
Mas. 42.7
Mkwiyo wanu utsamira pa ine,
ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.
8Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;
munandiika ndiwakhalire chonyansa.
Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine.
9 #
Yob. 11.13; Mas. 86.3 Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga:
Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;
nditambalitsira manja anga kwa Inu.
10 #
Yes. 38.18
Kodi mudzachitira akufa zodabwitsa?
Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?
11Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi,
chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko?
12Zodabwitsa zanu zidadziwika mumdima kodi,
ndi chilungamo chanu m'dziko la chiiwaliko?
13 #
Mas. 5.3; 119.147 Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova,
ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.
14 #
Mas. 43.2; 13.1 Yehova mutayiranji moyo wanga?
Ndi kundibisira nkhope yanu?
15Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;
posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.
16Kuzaza kwanu kwandimiza;
zoopsa zanu zinandiononga.
17Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;
zinandizinga pamodzi.
18Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa,
odziwana nane akhala kumdima.
Currently Selected:
MASALIMO 88: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi