MASALIMO 87
87
Yehova akonda Ziyoni
Salimo la ana a Kora. Nyimbo.
1Maziko ake ali m'mapiri oyera.
2 #
Mas. 78.67-68
Yehova akonda zipata za Ziyoni
koposa zokhalamo zonse za Yakobo.
3 #
Yes. 60
Mudzi wa Mulungu, inu,
akunenerani zakukulemekezani.
4Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine;
taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi;
uyu anabadwa komweko.
5Ndipo adzanena za Ziyoni,
uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo;
ndipo Wam'mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa.
6 #
Ezk. 13.9
Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu,
uyu anabadwa komweko.
7 #
Yes. 12.3
Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati,
akasupe anga onse ali mwa inu.
Currently Selected:
MASALIMO 87: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi