MASALIMO 86
86
Davide apempha Mulungu kolimba amlanditse
Pemphero la Davide
1Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe;
pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.
2Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;
Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.
3 #
Mas. 57.1
Mundichitire chifundo, Ambuye;
pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.
4Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;
pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.
5 #
Yow. 2.13
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,
ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
6Tcherani khutu pemphero langa, Yehova;
nimumvere mau a kupemba kwanga.
7 #
Mas. 50.15
Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;
popeza mudzandivomereza.
8 #
Eks. 15.11
Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;
ndipo palibe ntchito zonga zanu.
9 #
Yes. 66.23; Chiv. 15.4 Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye;
nadzalemekeza dzina lanu.
10 #
Deut. 6.4; Mrk. 12.29 Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa;
Inu ndinu Mulungu, nokhanu.
11 #
Mas. 25.2, 5 Mundionetse njira yanu, Yehova;
ndidzayenda m'choonadi chanu,
muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
12Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga,
ndi mtima wanga wonse;
ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
13 #
Mas. 116.8
Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu;
ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
14Mulungu, odzikuza andiukira,
ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,
ndipo sanaike Inu pamaso pao.
15 #
Eks. 34.6; Neh. 9.17 Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo,
wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
16 #
Mas. 25.16
Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo;
mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,
ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17Mundichitire chizindikiro choti chabwino;
kuti ondida achione, nachite manyazi,
popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.
Currently Selected:
MASALIMO 86: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi