YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 85

85
Akumbutsa Mulungu madalitso akale, apempha awabwereze
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la ana a Kora.
1 # Ezr. 1.11 Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova;
munabweza ukapolo wa Yakobo.
2 # Mas. 32.1 Munachotsa mphulupulu ya anthu anu,
munafotsera zolakwa zao zonse.
3Munabweza kuzaza kwanu konse;
munabwerera kumkwiyo wanu wotentha.
4Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu,
nimuletse udani wanu wa pa ife.
5 # Mas. 74.1 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?
Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?
6 # Hab. 3.2 Kodi simudzatipatsanso moyo,
kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?
7Tionetseni chifundo chanu, Yehova,
tipatseni chipulumutso chanu.
8 # Hab. 2.1; Zek. 9.10 Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova;
pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake,
ndi okondedwa ake;
koma asabwererenso kuchita zopusa.
9 # Yes. 46.13 Indedi chipulumutso chake chili pafupi
ndi iwo akumuopa Iye;
kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.
10 # Yes. 32.17 Chifundo ndi choonadi zakomanizana;
chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.
11 # Yes. 45.8 Choonadi chiphukira m'dziko;
ndi chilungamo chasuzumira chili m'mwamba.
12 # Mas. 67.6 Inde Yehova adzapereka zokoma;
ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.
13 # Mas. 89.14 Chilungamo chidzamtsogolera;
nichidzamkonzera mapazi ake njira.

Currently Selected:

MASALIMO 85: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 85