YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 84

84
Okhala m'nyumba ya Yehova ndiwo amwai
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Gititi; Salimo la ana a Kora.
1 # Mas. 27.4 Pokhala Inu mpotikonda ndithu,
Yehova wa makamu!
2 # Mas. 42.1-2 Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova;
mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.
3Mbawanso inapeza nyumba,
ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake,
pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu,
mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
4 # Mas. 65.4 Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu;
akulemekezani chilemekezere.
5Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu;
mumtima mwake muli makwalala a ku Ziyoni.
6Popyola chigwa cha kulira misozi achiyesa cha akasupe;
inde mvula ya chizimalupsa ichidzaza ndi madalitso.
7 # Yob. 17.9 Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,
aoneka pamaso pa Mulungu m'Ziyoni.
8Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa.
Tcherani khutu, Mulungu wa Yakobo.
9 # Gen. 15.1 Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu;
ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.
10Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma
koposa masiku ambirimbiri akukhala pena.
Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga,
kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.
11 # Yes. 60.19-20; Mat. 6.33; 7.11 Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa;
Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero;
sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
12 # Mas. 2.12 Yehova wa makamu,
wodala munthu wakukhulupirira Inu.

Currently Selected:

MASALIMO 84: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in