YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 83

83
Amitundu apangana kuononga Aisraele. Apempha Mulungu awalanditse
Nyimbo. Salimo la Asafu.
1 # Mas. 109.1 Mulungu musakhale chete;
musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.
2 # Mac. 4.25 Pakuti taonani, adani anu aphokosera,
ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.
3Apangana mochenjerera pa anthu anu,
nakhalira upo pa obisika anu.
4 # Est. 3.6, 9 Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;
ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.
5Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;
anachita chipangano cha pa Inu.
6Mahema a Edomu ndi a Aismaele;
Mowabu ndi Ahagiri;
7Gebala ndi Amoni ndi Amaleke;
Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m'Tiro.
8Asiriya anaphatikana nao;
anakhala dzanja la ana a Loti.
9 # Num. 31.7; Ower. 4.15, 24 Muwachitire monga munachitira Midiyani;
ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,
10amene anaonongeka ku Endori;
anakhala ngati ndowe ya kumunda.
11 # Ower. 7.25; 8.5-21 Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;
mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna,
12amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu.
13Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;
ngati ziputu zomka ndi mphepo.
14Monga moto upsereza nkhalango,
ndi monga lawi liyatsa mapiri.
15Momwemo muwatsate ndi namondwe,
nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu.
16 # Mas. 35.4, 26 Achititseni manyazi pankhope pao;
kuti afune dzina lanu, Yehova.
17Achite manyazi, naopsedwe kosatha;
ndipo asokonezeke, naonongeke.
18Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,
ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

Currently Selected:

MASALIMO 83: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 83