YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 82

82
Oweruza aweruza bwino
Salimo la Asafu.
1Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,
aweruza pakati pa milungu.
2 # Deut. 1.17; Miy. 18.5 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,
ndi kusamalira nkhope ya oipa?
3 # Yer. 22.3 Weruzani osauka ndi amasiye;
weruzani molungama ozunzika ndi osowa.
4Pulumutsani osauka ndi aumphawi;
alanditseni m'dzanja la oipa.
5 # Mik. 3.1-2 Sadziwa, ndipo sazindikira;
amayendayenda mumdima;
maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6 # Yoh. 10.34 Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,
ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.
7Komatu mudzafa monga anthu,
ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.
8 # Mas. 2.8 Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;
pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.

Currently Selected:

MASALIMO 82: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in