MASALIMO 82
82
Oweruza aweruza bwino
Salimo la Asafu.
1Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,
aweruza pakati pa milungu.
2 #
Deut. 1.17; Miy. 18.5 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,
ndi kusamalira nkhope ya oipa?
3 #
Yer. 22.3
Weruzani osauka ndi amasiye;
weruzani molungama ozunzika ndi osowa.
4Pulumutsani osauka ndi aumphawi;
alanditseni m'dzanja la oipa.
5 #
Mik. 3.1-2
Sadziwa, ndipo sazindikira;
amayendayenda mumdima;
maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6 #
Yoh. 10.34
Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,
ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.
7Komatu mudzafa monga anthu,
ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.
8 #
Mas. 2.8
Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;
pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.
Currently Selected:
MASALIMO 82: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi