YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 87

87
Yehova akonda Ziyoni
Salimo la ana a Kora. Nyimbo.
1Maziko ake ali m'mapiri oyera.
2 # Mas. 78.67-68 Yehova akonda zipata za Ziyoni
koposa zokhalamo zonse za Yakobo.
3 # Yes. 60 Mudzi wa Mulungu, inu,
akunenerani zakukulemekezani.
4Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine;
taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi;
uyu anabadwa komweko.
5Ndipo adzanena za Ziyoni,
uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo;
ndipo Wam'mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa.
6 # Ezk. 13.9 Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu,
uyu anabadwa komweko.
7 # Yes. 12.3 Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati,
akasupe anga onse ali mwa inu.

Currently Selected:

MASALIMO 87: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 87