YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 79

79
Yerusalemu apasuka, apempha Mulungu awathandize
Salimo la Asafu.
1 # 2Maf. 25.9-10 Mulungu, akunja alowa m'cholandira chanu;
anaipsa Kachisi wanu woyera;
anachititsa Yerusalemu bwinja.
2 # Deut. 28.26 Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhale
chakudya cha mbalame za mlengalenga,
nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zilombo za m'dziko.
3 # Yer. 14.16 Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu;
ndipo panalibe wakuwaika.
4Takhala chotonza cha anansi athu,
ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.
5 # Mas. 74.1 Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?
Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?
6 # Yer. 10.25; Chiv. 16.1 Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,
ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.
7Pakuti anathera Yakobo,
napasula pokhalira iye.
8 # Yes. 64.9 Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu;
nsoni zokoma zanu zitipeze msanga,
pakuti tafooka kwambiri.
9 # 2Mbi. 14.11 Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu,
chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu;
ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu,
chifukwa cha dzina lanu.
10 # Mas. 42.10 Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao?
Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa
kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu.
11 # Eks. 3.7; Mas. 102.20 Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu;
monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale.
12 # Yes. 65.6-7 Ndipo anansi athu amene anatonza Inu
muwabwezere chotonza chao,
kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.
13 # Mas. 95.7 Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu
tidzakuyamikani kosatha;
tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.

Currently Selected:

MASALIMO 79: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 79