YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 80

80
Apempha Mulungu alanditse anthu ake m'chisautso chao
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Syosyanimu; lochita mboni; Salimo la Asafu.
1 # Eks. 25.20, 22; Mas. 23.1 Mbusa wa Israele, tcherani khutu;
inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa;
inu wokhala pa akerubi, walitsani.
2 # Num. 2.18-23 Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase,
ndipo mutidzere kutipulumutsa.
3 # Num. 6.25 Mutibweze, Mulungu;
nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.
4Yehova, Mulungu wa makamu,
mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?
5 # Mas. 42.3 Munawadyetsa mkate wa misozi,
ndipo munawamwetsa misozi yambiri.
6Mutiika kuti atilimbirane anzathu;
ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha.
7 # Mas. 80.3, 19 Mulungu wa makamu, mutibweze;
nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.
8 # Yes. 5.1, 7 Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito,
munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.
9Mudasoseratu pookapo,
idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko.
10Mthunzi wake unaphimba mapiri,
ndi nthambi zake zikunga mikungudza ya Mulungu.
11Unatambalitsa mphanda zake mpaka kunyanja,
ndi mitsitsi yake kufikira ku Mtsinje.
12 # Yes. 5.5 Munapasuliranji maphambo ake,
kotero kuti onse akupita m'njira atcherako?
13Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba,
ndi nyama za kuchidikha ziudya.
14 # Yes. 63.15 Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu;
suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,
15ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka,
ndi mphanda munadzilimbikitsira.
16Unapserera ndi moto, unadulidwa;
aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.
17 # Mas. 89.20-21 Dzanja lanu likhale pa munthu wa pa dzanja lamanja lanu;
pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.
18Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani;
titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.
19 # Mas. 80.3, 7 Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu;
nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

Currently Selected:

MASALIMO 80: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 80