YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 78

78
Chikondi ndi chipiriro cha Mulungu cha pa Aisraele osakhulupirika
Chilangizo cha Asafu.
1 # Yes. 51.4 Tamverani, anthu anga, chilamulo changa;
tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga.
2 # Mat. 13.5 Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira;
ndidzatchula zinsinsi zoyambira kale.
3Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa,
ndipo makolo athu anatifotokozera.
4 # Deut. 4.9 Sitidzazibisira ana ao,
koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova,
ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.
5Anakhazika mboni mwa Yakobo,
naika chilamulo mwa Israele,
ndizo analamulira atate athu,
akazidziwitse ana ao;
6kuti mbadwo ukudzawo udziwe,
ndiwo ana amene akadzabadwa;
amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao.
7Ndi kuti chiyembekezo chao chikhale kwa Mulungu,
osaiwala zochita Mulungu,
koma kusunga malamulo ake ndiko.
8 # Eks. 32.9 Ndi kuti asange makolo ao,
ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu;
mbadwo wosakonza mtima wao,
ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu.
9Ana a Efuremu okhala nazo zida, oponya nao mauta,
anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo.
10 # 2Maf. 17.15 Sanasunga chipangano cha Mulungu,
nakana kuyenda m'chilamulo chake.
11Ndipo anaiwala zochita Iye,
ndi zodabwitsa zake zimene anawaonetsa.
12 # Eks. 7.12 Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao,
m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.
13 # Eks. 14.21 Anagawa nyanja nawapititsapo;
naimitsa madziwo ngati khoma.
14 # Eks. 13.21-22 Ndipo msana anawatsogolera ndi mtambo
ndi usiku wonse ndi kuunika kwa moto.
15 # Eks. 17.6; Num. 20.11 Anang'alula thanthwe m'chipululu,
ndipo anawamwetsa kochuluka monga m'madzi ozama.
16 # Eks. 17.6; Num. 20.11 Anatulukitsa mitsinje m'thanthwe,
inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje.
17 # Deut. 9.22 Koma anaonjeza kumchimwira Iye,
kupikisana ndi Wam'mwambamwamba m'chipululu.
18 # Eks. 16.2-8 Ndipo anayesa Mulungu mumtima mwao
ndi kupempha chakudya monga mwa kulakalaka kwao.
19Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu;
anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'chipululu?
20 # Eks. 17.6 Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako
ndi mitsinje inasefuka;
kodi adzakhozanso kupatsa mkate?
Kodi adzafunira anthu ake nyama?
21 # Num. 11.1-3 Chifukwa chake Yehova anamva, nakwiya;
ndipo anayatsa moto pa Yakobo,
ndiponso mkwiyo unakwera pa Israele.
22Popeza sanakhulupirire Mulungu,
osatama chipulumutso chake.
23Koma analamulira mitambo ili m'mwamba,
natsegula m'makomo a kumwamba.
24 # Eks. 16.4, 14; Yoh. 6.31 Ndipo anawavumbitsira mana, adye,
nawapatsa tirigu wa kumwamba.
25Yense anadya mkate wa angelo,
anawatumizira chakudya chofikira.
26 # Num. 11.20-33 Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa,
natsogoza mwera ndi mphamvu yake.
27Ndipo anawavumbitsira nyama ngati fumbi,
ndi mbalame zouluka ngati mchenga wa kunyanja.
28Ndipo anazigwetsa pakati pa misasa yao,
pozungulira pokhala iwo.
29Potero anadya nakhuta kwambiri;
ndipo anawapatsa chokhumba iwo.
30Asanathe nacho chokhumba chao,
chakudya chao chili m'kamwa mwao,
31pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira,
ndipo anapha mwa onenepa ao,
nagwetsa osankhika a Israele.
32 # Num. 14.16-17 Chingakhale ichi chonse anachimwanso,
osavomereza zodabwitsa zake.
33 # Num. 26.64-65 Potero anathera masiku ao ndi zopanda pake,
ndi zaka zao mwa mantha.
34Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye;
nabwerera, nafunitsitsa Mulungu.
35 # Deut. 32.30-31 Ndipo anakumbukira kuti Mulungu ndiye thanthwe lao,
ndi Mulungu Wam'mwambamwamba Mombolo wao.
36Koma anamsyasyalika pakamwa pao,
namnamiza ndi lilime lao.
37Popeza mtima wao sunakonzekera Iye,
ndipo sanakhazikike m'chipangano chake.
38 # Num. 14.18, 20 Koma Iye pokhala ngwa chifundo,
anakhululukira choipa, osawaononga;
nabweza mkwiyo wake kawirikawiri,
sanautse ukali wake wonse.
39 # Mas. 103.14 Ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu;
mphepo yopita yosabweranso.
40Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako,
nammvetsa chisoni m'chipululu.
41 # Num. 14.22; Mas. 78.20 Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu,
nachepsa Woyerayo wa Israele.
42Sanakumbukire dzanja lake,
tsikuli anawaombola kwa msautsi.
43Amene anaika zizindikiro zake m'Ejipito,
ndi zodabwitsa zake kuchidikha cha Zowani.
44 # Eks. 7.17-24 Nasanduliza nyanja yao mwazi,
ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa.
45 # Eks. 8.2-24 Anawatumizira pakati pao mitambo ya ntchentche zakuwatha;
ndi achule akuwaononga.
46 # Eks. 10.12-15 Ndipo anapatsa mphuchi dzinthu dzao,
ndi dzombe ntchito yao.
47 # Eks. 9.23-25 Anapha mphesa zao ndi matalala,
ndi mikuyu yao ndi chisanu.
48Naperekanso zoweta zao kwa matalala,
ndi ng'ombe zao kwa mphezi.
49Anawatumizira mkwiyo wake wotentha,
kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso,
ndizo gulu la amithenga ochita zoipa.
50Analambulira mkwiyo wake njira;
sanalekerere moyo wao usafe,
koma anapereka moyo wao kumliri.
51 # Eks. 12.29 Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito,
ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu.
52 # Mas. 77.20 Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa,
nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu.
53 # Eks. 14.19-20 Ndipo anawatsogolera mokhulupirika,
kotero kuti sanaope;
koma nyanja inamiza adani ao.
54Ndipo anawafikitsa kumalire a malo ake oyera,
kuphiri ili, dzanja lamanja lake lidaligula.
55 # Yos. 19.51 Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao,
nawagawira cholowa chao, ndi muyeso,
nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.
56 # Ower. 2.11-12 Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba,
osasunga mboni zake;
57koma anabwerera m'mbuyo,
nachita zosakhulupirika monga makolo ao,
anapatuka ngati uta wolenda.
58 # 1Maf. 12.31 Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao,
namchititsa nsanje ndi mafano osema.
59Pakumva ichi Mulungu, anakwiya,
nanyozatu Israele;
60 # 1Sam. 4.10-11, 21 ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo,
chihemacho adachimanga mwa anthu;
61napereka mphamvu yake m'ukapolo,
ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi.
62Naperekanso anthu ake kwa lupanga;
nakwiya nacho cholandira chake.
63Moto unapsereza anyamata ao;
ndi anamwali ao sanalemekezeke.
64 # 1Sam. 22.18 Ansembe ao anagwa ndi lupanga;
ndipo amasiye ao sanachite maliro.
65Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo;
ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo.
66Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo;
nawapereka akhale otonzeka kosatha.
67Tero anakana hema wa Yosefe;
ndipo sanasankhe fuko la Efuremu;
68 # Mas. 87.2 koma anasankha fuko la Yuda,
Phiri la Ziyoni limene analikonda.
69 # 1Maf. 6 Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri,
monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha.
70 # 1Sam. 16.11-12 Ndipo anasankha Davide mtumiki wake,
namtenga kumakola a nkhosa.
71 # 2Sam. 5.2 Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa,
awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholandira chake.
72 # 1Maf. 9.4 Potero anawaweta monga mwa mtima wake wangwiro;
nawatsogolera ndi luso la manja ake.

Currently Selected:

MASALIMO 78: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in