YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 77

77
Achita nkhawa pokumbuka zochita Mulungu, koma alimbika mtima pokumbuka zina adazichita Iye
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Yedutuni; Salimo la Asafu.
1Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga;
kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu.
2 # Mas. 50.15 Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye.
Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka;
mtima wanga unakana kutonthozedwa.
3Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika;
ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.
4Mundikhalitsa maso;
ndigwidwa mtima wosanena kanthu.
5 # Deut. 32.7 Ndinaganizira masiku akale,
zaka zakalekale.
6 # Mas. 42.8; Mali. 3.40 Ndikumbukira nyimbo yanga usiku;
ndilingalira mumtima mwanga;
mzimu wanga unasanthula.
7 # Mas. 74.1 Kodi Ambuye adzataya nthawi yonse?
Osabwerezanso kukondwera nafe.
8 # Aro. 9.6 Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi?
Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse?
9 # Yes. 49.15 Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo?
Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?
10Ndipo ndinati, Chindilaka ichi;
koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.
11 # Mas. 143.5 Ndidzakumbukira zimene adazichita Yehova;
inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zoyambira kale.
12Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse,
ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.
13Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu;
Mulungu wamkulu ndani monga Mulungu?
14Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa;
munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.
15 # Eks. 6.6 Munaombola anthu anu ndi mkono wanu,
ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.
16 # Eks. 14.21 Madziwo anakuonani Mulungu;
anakuonani madziwo; anachita mantha,
zozama zomwe zinanjenjemera.
17Makongwa anatsanula madzi;
thambo lidamvetsa liu lake;
mivi yanu yomwe inatulukira.
18Liu la bingu lanu linatengezanatengezana;
mphezi zinaunikira ponse pali anthu;
dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 # Hab. 3.15 Njira yanu inali m'nyanja,
koyenda Inu nku madzi aakulu,
ndipo mapazi anu sanadziwike.
20 # Eks. 13.21; Yes. 63.11-12 Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa,
ndi dzanja la Mose ndi Aroni.

Currently Selected:

MASALIMO 77: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 77