YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 76

76
Ulemerero ndi mphamvu ya Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Salimo la Asafu. Nyimbo.
1Mulungu adziwika mwa Yuda,
dzina lake limveka mwa Israele.
2 # Gen. 14.18 Msasa wake unali m'Salemu,
ndipo pokhala Iye m'Ziyoni.
3 # Ezk. 39.9 Pomwepo anathyola mivi ya pauta;
chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.
4Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka
wakuposa mapiri muli achifwamba.
5Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao;
amuna onse amphamvu asowa manja ao.
6 # Eks. 15.1, 21 Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,
galeta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo.
7 # Nah. 1.6 Inu ndinu woopsa;
ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?
8 # Ezk. 38.19-20 Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba;
dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete,
9pakuuka Mulungu kuti aweruze,
kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.
10 # Eks. 9.16 Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani;
chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.
11 # Mas. 50.14 Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;
onse akumzinga abwere nacho chopereka
cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.
12Iye adzadula mzimu wa akulu;
akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi.

Currently Selected:

MASALIMO 76: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 76