YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 75

75
Mulungu woweruza asiyanitsa pakati pa odzikuza ndi olungama
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Altasyeti; Salimo la Asafu. Nyimbo.
1Tikuyamikani Inu, Mulungu;
tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi;
afotokozera zodabwitsa zanu.
2Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika.
3Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;
ndinachirika mizati yake.
4Ndinati kwa odzitamandira,
musamachita zodzitamandira;
ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
5musamakwezetsa nyanga yanu;
musamalankhula ndi khosi louma.
6Pakuti kukuzaku sikuchokera kum'mawa,
kapena kumadzulo, kapena kuchipululu.
7 # Mas. 50.6; 1Sam. 2.7 Pakuti Mulungu ndiye woweruza;
achepsa wina, nakuza wina.
8 # Mas. 60.3 Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho;
ndi vinyo wake achita thovu;
chidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako.
Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa
nadzagugudiza nsenga zake.
9Koma ine ndidzalalikira kosalekeza,
ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo.
10 # Mas. 89.17; Yer. 48.25 Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa;
koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.

Currently Selected:

MASALIMO 75: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 75