YouVersion Logo
Search Icon

MASALIMO 74

74
Malo oyera adetsedwa. Apempha Mulungu akumbuke chipangano chao
Chilangizo cha Asafu.
1 # Mas. 44.9, 23; 95.7 Mulungu, munatitayiranji chitayire?
Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?
2 # Eks. 15.16 Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale,
umene munauombola ukhale fuko la cholandira chanu;
Phiri la Ziyoni limene mukhalamo.
3Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha,
zoipa zonse adazichita mdani m'malo opatulika.
4Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu;
aika mbendera zao zikhale zizindikiro.
5Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango.
6 # 1Maf. 6.18, 29, 32, 35 Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zake zonse
ndi nkhwangwa ndi nyundo.
7 # 2Maf. 25.9 Anatentha malo anu opatulika;
anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu.
8Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi;
anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo.
9 # 1Sam. 3.1 Sitiziona zizindikiro zathu;
palibenso mneneri;
ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.
10Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu?
Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?
11Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu?
Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu.
12 # Mas. 44.4 Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale,
wochita zakupulumutsa pakati pa dziko lapansi.
13 # Eks. 14.21 Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu;
mudaswa mitu ya zoopsa za m'madzi.
14Mudaphwanya mitu ya Leviyatani;
mudampereka akhale chakudya cha zilombo za m'chipululu.
15 # Yos. 3.13-17 Mudagawa kasupe ndi mtsinje;
mudaphwetsa mitsinje yaikulu.
16 # Gen. 1.14-19 Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu,
munakonza kuunika ndi dzuwa.
17 # Gen. 8.22 Munaika malekezero onse a dziko lapansi;
munalenga dzinja ndi malimwe.
18Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza,
ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.
19Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo;
musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse.
20 # Gen. 17.7; Yer. 33.20-21 Samalirani chipanganocho;
pakuti malo a mdima a m'dziko adzala ndi zokhalamo chiwawa.
21Okhalira mphanthi asabwere nao manyazi;
wozunzika ndi waumphawi alemekeze dzina lanu.
22Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha;
kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.
23Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu;
kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakwera kosaleka.

Currently Selected:

MASALIMO 74: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for MASALIMO 74