YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 10

10
Pangano lokhazikika pakati pa anthu ndi Mulungu
1Okomera chizindikiro tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya, 2Seraya, Azariya, Yeremiya, 3Pasuri, Amariya, Malikiya, 4Hatusi, Sebaniya, Maluki, 5Harimu, Meremoti, Obadiya, 6Daniele, Ginetoni, Baruki, 7Mesulamu, Abiya, Miyamini, 8Maaziya, Biligai, Semaya, ndiwo ansembe. 9Ndi Alevi ndiwo Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa ana a Henadadi, Kadimiyele; 10ndi abale ao: Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, 11Mika, Rehobu, Hasabiya, 12Zakuri, Serebiya, Sebaniya, 13Hodiya, Bani, Beninu. 14Akulu a anthu: Parosi, Pahatimowabu, Elamu, Zatu, Bani, 15Buni, Azigadi, Bebai, 16Adoniya, Bigivai, Adini, 17Atere, Hezekiya, Azuri, 18Hodiya, Hasumu, Bezai, 19Harifi, Anatoti, Nebai, 20Magapiyasi, Mesulamu, Heziri, 21Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, 22Pelatiya, Hanani, Anaya, 23Hoseya, Hananiya, Hasubu, 24Halohesi, Piliha, Sobeki, 25Rehumu, Hasabuna, Maaseiya, 26ndi Ahiya, Hanani, Anani, 27Maluki, Harimu, Baana. 28#Ezr. 2.36-43Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira, 29#Mas. 119.106amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake; 30#Ezr. 9.12, 14ndi kuti sitidzapereka ana athu akazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu amuna ana ao akazi; 31#Eks. 20.10; 23.10-11; Deut. 15.1-2; Neh. 13.15-22ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao tsiku la Sabata, kapena dzuwa lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse. 32Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu; 33#Num. 28—29kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu. 34#Neh. 13.31Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo; 35#Num. 18.12-26ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova; 36ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu; 37ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife. 38Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma. 39#Deut. 12.6, 11; Neh. 13.11-12Pakuti ana a Israele ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.

Currently Selected:

NEHEMIYA 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in