YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 11

11
Ena akhala m'Yerusalemu, ena m'midzi ina
1Ndipo akulu a anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'midzi ina. 2#Ower. 5.9Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala m'Yerusalemu.
3 # 1Mbi. 9.2-34 Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomoni. 4Ndipo m'Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi; 5ndi Maaseiya mwana wa Baruki, mwana wa Kolihoze, mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribu, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni. 6Ana onse a Perezi okhala m'Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu. 7Ndi ana a Benjamini ndi awa: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itiyele, mwana wa Yesaya. 8Ndi wotsatana naye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. 9Ndi Yowele mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mudzi. 10Mwa ansembe: Yedaya mwana wa Yoyaribu, Yakini, 11Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu; 12ndi abale ao ochita ntchito ya m'nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya; 13ndi abale ake akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasisai mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri; 14ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiele mwana wa Hagedolimu. 15Ndi mwa Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni; 16ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akulu a Alevi, anayang'anira ntchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu; 17ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni. 18Alevi onse m'mudzi wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai. 19Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. 20Ndi Aisraele otsala ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'cholowa chake. 21Koma Anetini anakhala m'Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini. 22Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu. 23Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake. 24Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo. 25Ndi ana ena a Yuda anakhala m'midzi ya kuminda yao, m'Kiriyati-Ariba ndi milaga yake, ndi m'Diboni ndi milaga yake, ndi m'Yekabizeele ndi midzi yake, 26ndi m'Yesuwa, ndi m'Molada, ndi Betepeleti, 27ndi m'Hazara-Suwala, ndi m'Beereseba ndi milaga yake, 28ndi m'Zikilagi, ndi m'Mekona ndi milaga yake, 29ndi m'Enirimoni, ndi m'Zora, ndi m'Yaramuti, 30Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yake, Azeka ndi milaga yake. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka chigwa cha Hinomu. 31Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi milaga yake, 32pa Anatoti, Nobi, Ananiya, 33Hazori, Rama, Gitaimu, 34Hadidi, Zeboimu, Nebalati, 35Lodi, ndi Ono, chigwa cha amisiri. 36Ndi magawo a Levi anakhala ena ku Yuda, ndi ena ku Benjamini.

Currently Selected:

NEHEMIYA 11: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in