NEHEMIYA 9
9
Msonkhano wa kusala ndi kupemphera
1 #
Neh. 8.2
Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israele anasonkhana ndi kusala, ndi kuvala chiguduli, ndipo anali ndi fumbi. 2#Ezr. 10.11; Neh. 13.3, 30Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao. 3#Neh. 8.7-8Naimirira poima pao, nawerenga m'buku la chilamulo cha Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anawulula, napembedza Yehova Mulungu wao. 4Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau akulu kwa Yehova Mulungu wao. 5Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse. 6#Mas. 86.10; 36.6Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu. 7#Gen. 12.1Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa m'Uri wa Ababiloni, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu; 8#Gen. 15.6, 18ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama. 9#Eks. 3.7Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira, 10#Eks. 7—14nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino. 11Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba. 12Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo. 13#Eks. 19—20Munatsikiranso pa phiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera m'Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma; 14ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu; 15#Eks. 16.14-15; Eks. 17.6; Num. 20.9-11; Deut. 1.8; Yoh. 6.31ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa. 16#Mas. 106.6-8Koma iwo ndi makolo athu anachita modzikuza, naumitsa khosi lao, osamvera malamulo anu, 17nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiya. 18#Eks. 32.4, 8Ngakhale apa atadzipangira mwanawang'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu; 19koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiya m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokera usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo. 20#Num. 11.17Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamana mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao. 21#Deut. 8.3-4Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinatha, ndi mapazi ao sanatupe. 22#Num. 21.21-35Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. 23Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao. 24#Yos. 9.15-22Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao. 25Ndipo analanda midzi yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu. 26#Mas. 50.16-17Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu. 27#Ower. 2.14-18Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva m'Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao. 28#Ower. 3.11-12; 4.1; 5.31; 6.1; Mas. 106.43Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m'dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva m'Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu; 29#Neh. 9.16ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera. 30#Yes. 5.5; 42.24; Mac. 7.51-52Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko. 31#Yer. 4.27Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawatha, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo. 32#Eks. 34.6-7Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino. 33#Mas. 106.6; 119.137Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa; 34ndi mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunge chilamulo chanu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawachitira umboni nazo. 35Popeza sanatumikire Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wochuluka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikulu ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerere kuleka ntchito zao zoipa. 36#Ezr. 9.9Tapenyani, ife lero ndife akapolo, ndi dzikoli mudalipereka kwa makolo athu kudya zipatso zake ndi zokoma zake, taonani, ife ndife akapolo m'menemo. 37#Deut. 28.33, 48, 51Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu. 38#Ezr. 10.3Ndipo mwa ichi chonse tichita pangano lokhazikika, ndi kulilemba, ndi akulu athu, Alevi athu, ndi ansembe athu, alikomera chizindikiro.
Currently Selected:
NEHEMIYA 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi