NEHEMIYA 8
8
Ezara awerengera anthu buku la chilamulo
1 #
Ezr. 7.6
Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele. 2#Deut. 31.11-12; Lev. 23.24Ndipo Ezara wansembe anabwera nacho chilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri. 3Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo. 4Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu. 5#1Maf. 8.14Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka. 6#Eks. 4.31; 2Mbi. 20.18; Mas. 28.2; 1Tim. 2.8Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi. 7#2Mbi. 17.7-9Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao. 8#2Mbi. 17.7-9Nawerenga iwo m'buku m'chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa chowerengedwacho. 9#Num. 29.1; Mlal. 3.4Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamachita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a chilamulo. 10#Est. 9.19, 22; Chiv. 11.10Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu. 11Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli chete; pakuti lero ndi lopatulika; musamachita chisoni. 12#Neh. 8.10Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.
Chikondwerero cha Misasa
13Ndipo m'mawa mwake akulu a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a chilamulo. 14#Lev. 23.34, 40, 42Napeza munalembedwa m'chilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israele azikhala m'misasa pa chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri, 15ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi m'Yerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa. 16Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la chipata cha Efuremu. 17#2Mbi. 30.21Ndi msonkhano wonse wa iwo otuluka m'ndende anamanga misasa, nakhala m'misasamo; pakuti chiyambire masiku a Yoswa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israele sanatero. Ndipo panali chimwemwe chachikulu. 18#Deut. 31.10-11; Lev. 23.36Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.
Currently Selected:
NEHEMIYA 8: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi