NEHEMIYA 7
7
Alonda adikira Yerusalemu
1 #
Neh. 6.1
Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi; 2#Eks. 18.21ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu. 3Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake. 4Mudziwo tsono ndi wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.
Maina a oyamba kubwerera kuchokera ku Babiloni
5Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo. 6#Ezr. 2.1-70Ana a dziko amene anakwera kuchokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa: 7ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisraele ndiwo: 8ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri. 9Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. 10Ana a Ara, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. 11Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi limodzi ndi asanu ndi atatu. 12Ana a Elamu, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai. 13Ana a Zatu, mazana asanu ndi atatu mphambu makumi anai kudza asanu. 14Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi. 15Ana a Binuyi, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu. 16Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. 17Ana a Azigadi, zikwi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi awiri ndi awiri. 18Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi, kudza asanu ndi awiri. 19Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri. 20Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu. 21Ana a Atere, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu. 22Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. 23Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai. 24Ana a Harifi, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri. 25Ana a Gibiyoni, makumi asanu ndi anai kudza asanu. 26Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza asanu ndi atatu. 27Amuna a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. 28Amuna a ku Betazimaveti, makumi anai kudza awiri. 29Amuna a ku Kiriyati-Yearimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu. 30Amuna a ku Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi. 31Amuna a ku Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri. 32Amuna a ku Betele ndi Ai, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu. 33Amuna a ku Nebo winayo, makumi asanu kudza awiri. 34Ana a Elamu winayo, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai. 35Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri. 36Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu. 37Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi. 38Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi anai kudza makumi atatu. 39Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu. 40Ana a Imeri, chikwi chimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. 41Ana a Pasuri, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri. 42Ana a Harimu, chikwi chimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri. 43A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyele, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai. 44Oimbira: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu. 45Odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu. 46Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 47ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni, 48ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai, 49ana a Hanani, ana a Gidele, ana a Gahara, 50ana a Reaya, ana a Rezini, ana a Nekoda, 51ana a Gazamu, ana a Uza, ana a Paseya, 52ana a Besai, ana a Meunimu, ana a Nefusesimu, 53ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 54ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa, 55ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 56ana a Neziya, ana a Hatifa. 57Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida, 58ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gidele, 59ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-Hazebaimu, ana a Amoni. 60Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri. 61Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele; 62ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri. 63Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao. 64Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe. 65Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu. 66Msonkhano wonse pamodzi ndiwo zikwi makumi anai ndi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi, 67osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri mphambu makumi anai kudza asanu ndi mmodzi. 68Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu; 69ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu ao zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.
Zopereka za akulu
70Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu. 71Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri. 72Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri, ndi malaya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri. 73Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi Anetini, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao.
Currently Selected:
NEHEMIYA 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi