YouVersion Logo
Search Icon

NEHEMIYA 6

6
Adani ayesa kunyenga ndi kuopsa Nehemiya
1 # Neh. 2.10, 19 Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata); 2anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane kumidzi ya ku Chigwa cha Ono; koma analingirira za kundichitira choipa. 3Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani? 4Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo. 5Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wake kwa ine kachisanu, ndi kalata wosatseka m'dzanja mwake; 6#Neh. 2.19m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa. 7Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi. 8Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako. 9Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
10Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane kunyumba ya Mulungu m'kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe. 11Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa m'Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo. 12#Ezk. 13.22Ndipo ndinazindikira kuti sanamtume Mulungu; koma ananena choneneracho pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera. 13Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza. 14#Neh. 13.29Mukumbukire, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa ntchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.
15Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri. 16#Mas. 126.1-2Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu. 17Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso akalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso akalata ake a Tobiya. 18Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya. 19Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine.

Currently Selected:

NEHEMIYA 6: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in