MARKO 3
3
Yesu achiritsa wa dzanja lopuwala
(Mat. 19.9-21; Luk. 6.6-11)
1Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lake lopuwala. 2Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu. 3Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati. 4Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete. 5Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake. 6#Mat. 22.16Ndipo Afarisi anatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.
7 #
Luk. 6.17
Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya, 8ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye. 9Ndipo anati kwa ophunzira ake, kuti kangalawa kamlinde Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye, 10pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze. 11#Luk. 4.41; Mat. 14.33Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. 12Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye.
Apatula ophunzira khumi ndi awiri
(Mat. 10.1-4)
13Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye. 14Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira, 15ndi kuti akhale nao ulamuliro wakutulutsa ziwanda. 16#Yoh. 1.42Ndipo Simoni anamutcha Petro; 17ndi Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo, iwo anawatcha Boaneje, ndiko kuti, Ana a bingu; 18ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani, 19ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye.
Za Yesu ndi Belezebulu
(Mat. 12.24-32; Luk. 11.14-23)
20 #
Mrk. 6.31
Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya. 21#Yoh. 10.20Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka. 22#Mat. 9.34Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda. 23Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana? 24Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika. 25Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, sikhoza kukhazikika nyumbayo, 26Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika. 27#Yes. 49.24Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake. 28#Luk. 12.10; 1Yoh. 5.16Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo; 29#Luk. 12.10; 1Yoh. 5.16koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha; 30pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.
Abale ake a Yesu
(Mat. 12.46-50; Luk. 8.19-21)
31Ndipo anadza amake ndi abale ake; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana. 32Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu. 33Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani? 34Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga. 35Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai.
Currently Selected:
MARKO 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi