MARKO 4
4
Fanizo la wofesa
(Mat. 13.1-18; Luk. 8.4-15)
1Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja. 2Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'chiphunzitso chake, 3Mverani: taonani, wofesa anatuluka kukafesa; 4ndipo kunali, m'kufesa kwake, zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndi mbalame zinadza ndi kuzitha kudya. 5Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya; 6ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata. 7Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nizitsamwitsa, ndipo sizinabala zipatso. 8#Akol. 1.6Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi. 9Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.
10 #
Luk. 8.9-10
Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo. 11Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo; 12#Yes. 6.9; Yoh. 12.40; Mac. 28.26; Aro. 11.8kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa. 13Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse?
Kumasulira kwa fanizo la wofesa
(Mat. 13.18-23)
14Wofesa afesa mau. 15Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo. 16Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera; 17ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mau, pomwepo akhumudwa. 18Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau, 19#1Tim. 6.9, 17ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso. 20Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.
Fanizo la nyali
(Luk. 8.16-18)
21 #
Mat. 5.15
Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaivundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa choikapo chake? 22#Mat. 10.26; Luk. 12.2Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe. 23#Mat. 11.15Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve. 24#Mat. 7.2; Luk. 6.38Ndipo ananena nao, Yang'anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu. 25#Mat. 13.12; Luk. 8.18Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kalikonse ali nako.
Fanizo la mbeu
26 #
Mat. 13.24
Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka; 27nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira. 28Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo. 29#Chiv. 14.15Pakutcha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.
Fanizo la mbeu yampiru
(Mat. 12.31-32; Luk. 13.18-19)
30Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani? 31Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ichepa ndi mbeu zonse za padziko, 32koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nichita nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake. 33#Yoh. 16.12Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva; 34ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.
Yesu aletsa namondwe
(Mat. 8.23-27; Luk. 8.22-25)
35Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina. 36Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye. 37Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala. 38Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife? 39Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu. 40Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi? 41Ndipo iwo anachita mantha akulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Currently Selected:
MARKO 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi