MARKO 2
2
Achiritsa wodwala manjenje
(Mat. 9.1-8; Luk. 5.18-26)
1Ndipo polowanso Iye m'Kapernao atapita masiku ena, kunamveka kuti ali m'nyumba. 2Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau. 3Ndipo anadza kwa Iye otenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anai. 4Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo. 5Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa. 6Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao, 7#Yes. 43.25Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu? 8Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu? 9Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende? 10Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira machimo pa dziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje), 11Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu. 12Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.
Yesu aitana Levi
(Mat. 9.9-13; Luk. 5.27-32)
13Ndipo anatulukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa. 14Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine. 15Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye. 16Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa. 17#Luk. 5.31-32; Luk. 19.10; 1Tim. 1.15Ndipo pamene Yesu anamva ichi, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.
Kudzikana kudya
(Mat. 9.14-17; Luk. 5.33-38)
18 #
Luk. 5.33
Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya? 19Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala. 20Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo. 21Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pena chimene choti chidzakonza chizomolapo, chatsopanocho chizomoka pa chakalecho, ndipo chiboo chikulapo. 22Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.
Yesu mwini Sabata
(Mat. 12.1-8; Luk. 6.1-5)
23 #
Deut. 23.25
Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda tsiku la Sabata; ndipo ophunzira ake poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu. 24Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la Sabata? 25#1Sam. 21.2-6Ndipo ananena nao, Simunawerenga konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye? 26#Eks. 29.32-33Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye? 27Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata; 28motero Mwana wa Munthu ali mwini tsiku la Sabata lomwe.
Currently Selected:
MARKO 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi