MARKO 1
1
Yohane Mbatizi
(Mat. 3.1-12; Luk. 3.1-18; Yoh. 1.6-8, 19-36; 3.23-32)
1 #
Mat. 14.33
Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. 2#Mala. 3.1Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri,
Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu,
amene adzakonza njira yanu.
3 #
Yes. 40.3; Luk. 3.4 Mau a wofuula m'chipululu,
konzani khwalala la Ambuye,
lungamitsani njira zake.
4 #
Luk. 3.3
Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo. 5Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao. 6Ndipo Yohane anavala ubweya wa ngamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wa kuthengo. 7#Mac. 13.25Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zake ine. 8#Mac. 1.5; 2.4Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.
Kubatizidwa ndi kuyesedwa kwa Yesu
(Mat. 3.13—4.11; Luk. 4.1-13)
9Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordani. 10#Luk. 3.21Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: 11#Mrk. 9ndipo mau anatuluka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino. 12#Luk. 4.3Ndipo pomwepo Mzimu anamkakamiza kunka kuchipululu. 13Ndipo anakhala m'chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zilombo, ndipo angelo anamtumikira.
Yesu aitana ophunzira ake oyamba
(Mat. 4.12-25; Yoh. 1.35-51)
14Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, 15#Agal. 4.4nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani Uthenga Wabwino.
16Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi. 17Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. 18#Mat. 19.27; Luk. 5.11Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye. 19Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, iwonso anali m'chombo nakonza makoka ao. 20Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata.
Achiritsidwa wogwidwa ndi chiwanda ku Kapernao
(Luk. 4.31-37)
21 #
Mat. 4.13
Ndipo iwo analowa m'Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa. 22#Mat. 7.28Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi. 23#Luk. 4.33Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye. 24#Mat. 8.29Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu. 25#Mrk. 1.34Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye. 26#Mrk. 9.20Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau akulu, unatuluka mwa iye. 27Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye. 28Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo.
Achiritsidwa mpongozi wa Petro ndi odwala ena
(Mat. 8.14-17; Luk. 4.38-41)
29Ndipo pomwepo, potuluka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane. 30Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye: 31ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.
32 #
Luk. 4.40
Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda. 33Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo. 34#Luk. 4.41Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.
35 #
Luk. 4.42
Ndipo m'mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko. 36Ndipo Simoni ndi anzake anali naye anamtsata, 37nampeza, nanena naye, Akufunani Inu anthu onse. 38#Yes. 61.1; Luk. 4.43; Yoh. 17.4Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, kumidzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imene. 39#Mat. 4.23; Luk. 4.44Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.
Yesu achiritsa wakhate
(Mat. 8.1-4; Luk. 5.12-14)
40Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza. 41Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa. 42Ndipo pomwepo khate linamchoka, ndipo anakonzedwa. 43Ndipo anamuuzitsa, namtulutsa pomwepo, 44#Lev. 14.3-4, 10; Luk. 5.14nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo. 45#5.15-16Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.
Currently Selected:
MARKO 1: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi