MARKO Mau Oyamba
Mau Oyamba
Buku la Marko likuyamba ndi mau akuti ichi ndi “chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu”. Yesu akumuonetsa monga munthu amene akuchita zinthu zambiri komanso waulamuliro. Ulamuliro wake ukuoneka mu chiphunzitso chake, mu mphamvu yake pa ziwanda ndi kuwakhululukira anthu machimo ao. Yesu akudzitchula kuti ndi Mwana wa Munthu, amene anabwera kudzapereka moyo wake kuti awapulumutse anthu ku machimo ao.
Marko akulemba mbiri ya Yesu mwachimvekere, mwachangu ndi motsindika kwambiri pa zimene Yesu anachita, osati pa mau ake kapena pa chiphunzitso chake. Atanena mwachidule za Yohane Mbatizi ndi za ubatizo wa Yesu, wolembayo akuthamangira kulemba za utumiki wa Yesu wa kuchiritsa ndi kuphunzitsa. Kenaka akutionetsa kuti omutsatira a Yesu amamumvetsetsa pamene adani ake anapitirira kumuda. Mitu yomaliza imakamba zimene Yesu anachita mu sabata yake yomaliza ya utumiki wake pansi pano, makamaka kupachikidwa pamtanda ndi kuukanso kwake.
Za mkatimu
Chiyambi cha Uthenga Wabwino 1.1-13
Utumiki wa Yesu ku Galileya 1.14—9.50
Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu 10.1-52
Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 11.1—15.47
Kuukanso kwa Yesu 16.1-8
Ambuye woukitsidwayo aonekera nakwera kumwamba 16.9-20
Currently Selected:
MARKO Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi