MIKA 6
6
Mulungu atsutsana ndi anthu ake chifukwa cha zoipa zao
1Tamverani tsono chonena Yehova: Nyamuka, tsutsana nao mapiri, ndi zitunda zimve mau ako. 2#Yes. 1.18Tamverani, mapiri inu, chitsutsano cha Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali nacho chitsutsano ndi anthu ake, ndipo adzatsutsana ndi Israele. 3#Yer. 2.5Anthu anga inu, ndakuchitirani chiyani? Ndakulemetsani ndi chiyani? Chitani umboni wonditsutsa. 4#Eks. 12.51Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu. 5#Num. 22.5; 25.1Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova. 6Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi? 7#2Maf. 16.3; Mas. 50.9; Yes. 1.11Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga? 8#Deut. 10.12; Yes. 1.17Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
9Mau a Yehova aitana mudzi, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika. 10#Deut. 25.13-16Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao? 11#Deut. 25.13-16Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga? 12#Yer. 9.3, 5, 8Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao. 13Chifukwa chake Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula chifukwa cha zochimwa zako. 14Udzadya koma osakhuta; ndi njala yako idzakhala pakati pako; ndipo udzachotsa koma osalanditsa; ndi ichi wachilanditsa ndidzachipereka kulupanga. 15#Deut. 28.38-40Udzafesa koma osacheka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo. 16#1Maf. 16.25-33Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda m'uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.
Currently Selected:
MIKA 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi