MIKA 5
5
1 #
Mat. 5.39; 27.30 Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.
Aneneratu za kubadwa kwa woweruza m'Israele
2 #
Mat. 2.6; Yoh. 1.1 Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza m'Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba. 3Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele. 4#Mas. 72.8; Yes. 40.11Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, m'ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi. 5#Zek. 9.10; Luk. 2.14Ndipo ameneyo adzakhala Mtendere; pamene a ku Asiriya adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu. 6Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu. 7Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu. 8Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa. 9Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.
10Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magaleta ako; 11ndipo ndidzaononga midzi ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse; 12ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi; 13#Zek. 13.2ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako. 14Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha midzi yako. 15#Mas. 149.7; 2Ate. 1.8Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera chilango mu mkwiyo waukali.
Currently Selected:
MIKA 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi