YouVersion Logo
Search Icon

MIKA 7

7
Za kuipa kwakukulu kwa Aisraele, ndi chifundo cha Mulungu
1 # Yes. 17.6 Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa. 2#Mas. 14.1, 3Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde. 3Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi. 4#2Sam. 23.6-7Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao. 5#Yer. 9.4Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako. 6#Mat. 10.21, 35-36Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amake, mpongozi aukira mpongozi wake; adani ake a munthu ndiwo a m'nyumba yake.
7 # Yes. 8.17; Mali. 3.25-26 Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera. 8#Mas. 27.1; Mali. 4.21Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga. 9#Mas. 37.6; Mali. 3.39Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake. 10#Mas. 35.26Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu. 11Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzachotsedwa kunka kutali. 12#Yes. 11.16Tsiku lomwelo adzadza kwa iwe, kuchokera ku Asiriya ndi midzi ya ku Ejipito, kuyambira ku Ejipito kufikira ku Mtsinje, ndi kuyambira kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuyambira kuphiri kufikira kuphiri. 13Koma dziko lidzakhala labwinja chifukwa cha iwo okhalamo, mwa zipatso za machitidwe ao.
14 # Mas. 23.4 Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pa zokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye m'Basani ndi m'Giliyadi masiku a kale lomwe. 15Monga masiku a kutuluka kwako m'dziko la Ejipito ndidzamuonetsa zodabwitsa. 16#Yes. 26.11Amitundu adzaona nadzachita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha. 17#Yes. 49.23Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe. 18#Eks. 15.11; 34.6-7Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo. 19#Yes. 38.17Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya. 20#Luk. 1.72-73Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.

Currently Selected:

MIKA 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in