YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 24

24
Yesu anenera zam'tsogolo. Chiyambi cha masautso
(Mrk. 13; Luk. 21.5-36)
1Ndipo Yesu anatuluka ku Kachisi; ndipo ophunzira ake anadza kudzamuonetsa chimangidwe cha Kachisiyo. 2#1Maf. 9.7; Luk. 19.44Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.
3 # Mrk. 13.3; 1Ate. 5.1 Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano? 4Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu. 5#Yer. 14.14; Yoh. 5.43Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri. 6Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike. 7Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti. 8Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.
9 # Mrk. 13.9; Mac. 4.2-3 Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa. 10Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake. 11#Mac. 20.29; 1Tim. 4.1Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri. 12Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusaweruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala. 13#Mrk. 13.13; Chiv. 2.10Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka. 14#Akol. 1.6, 23Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.
Chisautso chachikulu
15 # Dan. 9.27; 12.11; Mrk. 13.14 Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire) 16pomwepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri: 17iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake; 18ndi iye wa m'munda asabwere kutenga chofunda chake. 19#Luk. 23.29Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m'masiku awo! 20Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu, kapena pa Sabata; 21#Dan. 9.26; 12.1pakuti pomwepo padzakhala masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. 22#Yes. 65.8Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa. 23#Mrk. 13.21Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Khristu ali kuno, kapena uko musamvomereze; 24#Yoh. 6.37; Aro. 8.28-30; 2Ate. 2.8-10chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike. 25Chifukwa chake akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'chipululu; musamukeko. 26Onani, ali m'zipinda; musavomereze. 27#Luk. 17.24Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. 28#Luk. 17.37Kumene kulikonse uli mtembo, miimba idzasonkhanira konko.
Kudza kwake kwa Mwana wa Munthu
29 # Dan. 7.11-12; Yes. 13.9-10; Mrk. 13.24 Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka: 30#Dan. 7.13; Mat. 16.27; Mrk. 13.26ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. 31#Mat. 13.41; 1Ako. 15.52Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena. 32#Luk. 21.29Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; 33chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo. 34#Mat. 16.28; Mrk. 13.30Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa. 35#Yes. 51.6; Mrk. 13.31Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.
Awachenjeza adikire
36 # Mrk. 13.32; Mac. 1.7 Koma za tsiku ili ndi nthawi yake sadziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. 37#Gen. 6.7Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. 38Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa, 39Ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. 40#Luk. 17.34-35Pomwepo adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: 41awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. 42#Mrk. 13.33-37Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. 43#Luk. 12.39; 1Ate. 5.2Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe. 44#1Ate. 5.6Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.
Fanizo la akapolo awiri
(Luk. 12.42-48)
45 # Luk. 12.42; Mac. 20.28 Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake? 46Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. 47#Luk. 22.29Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zake zonse. 48Koma kapolo woipa akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa; 49nadzayamba kupanda akapolo anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera; 50mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye, 51#Mat. 8.12nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Currently Selected:

MATEYU 24: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in