Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa, Ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.