MATEYU 25
25
Fanizo la anamwali asanu ochenjera ndi asanu opusa
1 #
Chiv. 19.7
Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati. 2#Mat. 22.10Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. 3Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta; 4koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. 5#1Ate. 5.6Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo. 6Koma pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! Tulukani kukakomana naye. 7#Luk. 12.35Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao. 8Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima. 9Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha. 10#Luk. 13.25Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo. 11#Mat. 7.21-23Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. 12Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani. 13#Mat. 24.42-44Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake.
Fanizo la ndalama za matalente
(Luk. 19.11-27)
14 #
Mat. 21.33
Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. 15#Aro. 12.6Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye. 16Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu. 17Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri. 18Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake. 19Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi. 20Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu. 21#Mat. 24.47; Luk. 12.44Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. 22Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri. 23Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. 24Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza; 25ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. 26Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza; 27chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. 28Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. 29#Mat. 13.12Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. 30#Mat. 24.51Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Moyo wosatha ndi kulanga kosatha
31 #
Mrk. 8.38; 1Ate. 4.16 Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake: 32#Mat. 13.49; Aro. 14.10ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; 33nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere. 34#Mrk. 10.40Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: 35#Yes. 58.7; Aheb. 13.2pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; 36#2Tim. 1.16; Yak. 2.15-16wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine. 37Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? 38Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? 39Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu? 40#Miy. 19.17; Mrk. 9.41Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine. 41#Luk. 13.27Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake: 42pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine: 43ndinali mlendo, ndipo simunandilandira Ine; wamaliseche ndipo simunandiveka Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona Ine. 44Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu? 45#Miy. 14.31Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine. 46#Yoh. 5.28; Aro. 2.6-8Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.
Currently Selected:
MATEYU 25: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi