YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 23

23
Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi
1Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ake, 2#Mala. 2.7nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose; 3#Aro. 2.19-22chifukwa chake zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zao; pakuti iwo amalankhula, koma samachita. 4#Mac. 15.10Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao. 5#Mat. 6.1-2, 5, 16; Num. 15.38Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje, 6#Mrk. 12.38-39nakonda malo a ulemu pamaphwando, ndi mipando ya ulemu m'masunagoge, 7#Mrk. 12.38-39ndi kulonjeredwa m'misika, ndi kutchedwa ndi anthu, Rabi. 8#Yak. 3.1Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. 9#Mala. 1.6Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. 10Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Khristu. 11#Mat. 20.26-27Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. 12#Miy. 15.33; Yak. 4.6Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.
13 # Luk. 11.52 Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.#23.13 Mabuku ena akale amaonjezerapo vesi 14 Muli ndi tsoka, inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumakongola chuma m'malo mwa amai amasiye, nkumawadyera chumacho, kwinaku nkumanyengezera kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha ichi, chilango chanu chidzakhala choopsa.
15Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa Gehena woposa inu kawiri.
16Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira. 17Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo? 18Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira. 19Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo? 20Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake. 21Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo. 22Ndipo wakulumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.
23 # Deut. 14.22; 1Sam. 15.22; Luk. 11.42 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. 24Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumeza ngamira.
25 # Mrk. 7.4 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa. 26Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.
27 # Luk. 11.44 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. 28Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.
29 # Luk. 11.47-48 Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama, 30ndi kuti, Ife tikadakhala m'masiku a makolo anthu, sitikadakhala oyanjana nao pa mwazi wa aneneri. 31Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri. 32Dzazani inu muyeso wa makolo anu. 33Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa Gehena? 34#Luk. 11.49-51Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina; 35#Gen. 4.4-8; Zek. 1.1; Luk. 11.49-51kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe. 36Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono.
37 # Luk. 13.34-35 Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafuna ai! 38#Luk. 13.34-35Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja. 39#Mas. 118.26; Luk. 13.34-35Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena,
Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.

Currently Selected:

MATEYU 23: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in