YouVersion Logo
Search Icon

MATEYU 22

22
Fanizo la ukwati
(Luk. 14.16-24)
1Ndipo Yesu anayankha, nalankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati, 2Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati, 3natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa kuukwati umene; ndipo iwo sanafune kudza. 4Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati. 5Koma iwo ananyalanyaza, nachoka, wina kumunda wake, wina kumalonda ake: 6ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha. 7Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao. 8#Mac. 13.46Pomwepo inanena kwa akapolo ake, Za ukwati tsopano zapsa, koma oitanidwawo sanayenera. 9Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeze, itanani kuukwatiku. 10#Mat. 12.47Ndipo akapolo ao anatulukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pachakudya. 11#Akol. 3.10-11Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala cha ukwati; 12nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mau. 13#Mat. 8.12Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano. 14#Mat. 20.16Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka.
Za kupereka msonkho kwa Kaisara
(Mrk. 12.13-17; Luk. 20.20-26)
15Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwake. 16Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu. 17Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai? 18Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu? 19Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka. 20Ndipo Iye anati kwa iwo, Ncha yani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake? 21#Aro. 13.7Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu. 22Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nachokapo.
Asaduki ndi kuuka kwa akufa
(Mrk. 12.18-27; Luk. 20.27-40)
23Tsiku lomwelo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye, 24nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu. 25Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwake mkazi wake; 26chimodzimodzi wachiwiri, ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiwiri. 27Ndipo pomalizira anamwaliranso mkaziyo. 28Chifukwa chake m'kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi awiriwo? Pakuti onse anakhala naye. 29#Yoh. 20.9Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu. 30#1Yoh. 3.2Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba. 31Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenga kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,
32 # Eks. 3.6, 16; Mrk. 12.26; Aheb. 11.16 Ine ndili Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki,
ndi Mulungu wa Yakobo?
Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo. 33#Mat. 7.28Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi chiphunzitso chake.
Lamulo lalikulu
(Mrk. 12.28-34; Luk. 10.25-27)
34Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana. 35Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa chilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati, 36Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndi liti la m'chilamulo? 37#Deut. 6.5; 10.12Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. 38Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. 39#Lev. 19.18; Aro. 13.9Ndipo lachiwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. 40#Mat. 7.12; Mrk. 12.31Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri.
Khristu ndiye Mwana wa Davide
(Mrk. 12.35-37; Luk. 20.41-44)
41Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa, 42nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide. 43Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena,
44 # Mas. 110.1; Mac. 2.34; 1Ako. 15.25 Ambuye ananena kwa Ambuye wanga,
ukhale pa dzanja lamanja langa,
kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.
45Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau. 46#Mrk. 12.34Ndipo sanalimbike mtima munthu aliyense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.

Currently Selected:

MATEYU 22: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in