Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka. Ndipo Iye anati kwa iwo, Ncha yani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake? Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.