MATEYU 21
21
Yesu alowa m'Yerusalemu
(Mrk. 11.1-10; Luk. 19.29-38; Yoh. 12.12-15)
1 #
Mrk. 11.1
Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri, 2nanena kwa iwo, Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nao kwa Ine. 3Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza. 4Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri kuti,
5 #
Zek. 9.9
Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni,
Taona, mfumu yako idza kwa iwe,
wofatsa ndi wokwera pa bulu,
ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.
6 #
Mrk. 11.4
Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza; 7#2Maf. 9.13nabwera ndi bulu ndi mwana wake, naika pa iwo zovala zao, nakhala Iye pamenepo. 8Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zovala zao panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m'njiramo. 9#Mas. 118.25-26Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana m'Kumwambamwamba! 10Ndipo m'mene adalowa m'Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu? 11#Luk. 7.16; Yoh. 6.14Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.
Yesu ayeretsa Kachisi kachiwiri
(Mrk. 11.15-18; Luk. 19.45-48; Yoh. 2.13-17)
12 #
Mrk. 11.11
Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; 13#Yes. 56.7; Yer. 7.11; Mrk. 11.17nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba. 14Ndipo anadza kwa Iye ku Kachisiko akhungu ndi opunduka miyendo, nachiritsidwa. 15Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima, 16#Mas. 8.2nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza? 17#Mrk. 11.11Ndipo Iye anawasiya, natuluka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.
Mkuyu wofota
(Mrk. 11.12-14, 19-24)
18 #
Mrk. 11.12
Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala. 19#Mrk. 11.13Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota. 20#Mrk. 11.20Ndipo ophunzira poona ichi anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga? 21#Mat. 17.20; Luk. 17.6Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa. 22#Mat. 7.7; Mrk. 11.24; Yoh. 14.14Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.
Ubatizo wa Yohane
(Mrk. 11.27-33; Luk. 20.1-8)
23 #
Mrk. 11.27; Mac. 4.7 Ndipo m'mene Iye analowa m'Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere? 24Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi: 25Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzake, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye? 26#Luk. 20.6Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri. 27Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.
Fanizo la ana amuna awiri
28Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa. 29Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita. 30Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite. 31#Luk. 7.29, 50Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. 32#Luk. 3.12-13Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvera iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalapa pambuyo pake, kuti mumvere iye.
Fanizo la olima munda wamphesa
(Mrk. 12.1-12; Luk. 20.9-19)
33 #
Mrk. 12.1
Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina. 34Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake. 35#Mac. 7.52; Aheb. 11.36-37Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala. 36Anatumizanso akapolo ena, akuchuluka oposa akuyambawa; ndipo anawachitira iwo momwemo. 37Koma pambuyo pake anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu. 38#Mas. 2.2, 8; Yoh. 11.53; Aheb. 1.2Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake. 39#Mat. 26.50Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha. 40Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani? 41#Mac. 28.28Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake. 42#Mas. 118.22-23; Yes. 28.16; Mrk. 12.10; Aef. 2.20Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenga konse m'malembo,
Mwala umene anaukana omanga nyumba
womwewu unakhala mutu wa pangodya:
Ichi chinachokera kwa Ambuye,
ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?
43 #
Mat. 8.12
Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake. 44#Zek. 12.3; Aro. 9.33Ndipo iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye. 45Ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi, pakumva mafanizo ake, anazindikira kuti alikunena za iwo. 46#Luk. 7.16; Yoh. 7.40Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, chifukwa anamuyesa mneneri.
Currently Selected:
MATEYU 21: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi